Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 62:1-12

Kwa wotsogolera nyimbo pa Yedutuni.* Nyimbo ya Davide. 62  Ndithudi, moyo wanga ukuyembekezera Mulungu modekha.+ Chipulumutso changa chidzachokera kwa iye.+   Iye ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa, malo anga okwezeka ndiponso achitetezo.+ Sindidzagwedezeka kwambiri.+   Kodi mudzayesayesa kufikira liti kuti muphe munthu amene mumadana naye?+ Nonsenu muli ngati khoma lopendekeka, khoma lamiyala limene akulikankha kuti ligwe.+   Iwo amapatsa munthu malangizo kuti amukope ndi kumutsitsa pamalo ake aulemu.+ Bodza limawasangalatsa.+ Iwo amadalitsa ndi pakamwa pawo, koma mumtima mwawo amatemberera.+ [Seʹlah.]   Ndithudi, yembekezera Mulungu modekha, iwe moyo wanga,+ Chifukwa chiyembekezo changa chichokera kwa iye.+   Ndithudi, iye ndi thanthwe langa ndi chipulumutso changa, malo anga okwezeka ndiponso achitetezo.+ Sindidzagwedezeka.+   Chipulumutso ndi ulemerero wanga zili mwa Mulungu.+ Iye ndi thanthwe langa lolimba ndi malo anga othawirako.+   Mukhulupirireni nthawi zonse, anthu inu.+ Mukhuthulireni za mumtima mwanu.+ Mulungu ndiye pothawirapo pathu.+ [Seʹlah.]   Ndithudi, ana a anthu ochokera kufumbi ali ngati mpweya,+ Ana a anthu ndi malo othawirako achinyengo.+ Onse pamodzi akaikidwa pasikelo ndi opepuka kuposa mpweya.+ 10  Musadalire chizolowezi chobera ena mwachinyengo,+ Ndipo musakhale wachabechabe chifukwa chochita uchifwamba.+ Ngati chuma chanu chachuluka, mtima wanu wonse usakhale pachumacho.+ 11  Kawiri konse ndamva kuti Mulungu wanena kuti,+ Mphamvu ndi za Mulungu.+ 12  Komanso kukoma mtima kosatha ndi kwanu, inu Yehova,+ Pakuti inu mumabwezera aliyense mogwirizana ndi ntchito zake.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Sl 39:Kamutu.