Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Masalimo 61:1-8

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe ndi zoimbira za zingwe. Salimo la Davide. 61  Inu Mulungu, imvani kulira kwanga kochonderera.+ Mvetserani pemphero langa mwatcheru.+   Mtima wanga ukalefuka, ndidzafuulira inu, kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+ Nditsogolereni ndi kundikweza pamwamba pa thanthwe lalitali kuposa msinkhu wanga.+   Pakuti inu mwakhala pothawirapo panga,+ Nsanja yolimba pamaso pa mdani.+   Ndidzakhala mlendo m’chihema chanu mpaka kalekale.+ Ndidzathawira m’malo obisalamo kunsi kwa mapiko anu.+ [Se′lah.]   Pakuti inu Mulungu, mwamvetsera malonjezo anga.+ Mwandipatsa cholowa chimene mwasungira anthu oopa dzina lanu.+   Mudzatalikitsa moyo wa mfumu.+ Zaka zake zidzachuluka kufanana ndi mibadwo yambirimbiri.+   Mfumuyo idzakhala pamaso pa Mulungu mpaka kalekale.+ Isonyezeni kukoma mtima kwanu kosatha ndi kuipatsa choonadi kuti zimenezi ziiteteze.+   Choncho ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu mpaka muyaya,+ Kuti ndikwaniritse malonjezo anga tsiku ndi tsiku.+

Mawu a M'munsi