Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 60:1-12

Kwa wotsogolera nyimbo pa Duwa la Chikumbutso. Mikitamu.* Salimo la Davide. Nyimbo yophunzitsira.+ Pa nthawi imene Davide anali pankhondo ndi Aramu-naharaimu ndi Aramu-Zoba, ndipo Yowabu anabwerera ndi kukapha Aedomu 12,000 m’chigwa cha Mchere.+ 60  Inu Mulungu, mwatitaya, ndipo mwasokoneza magulu athu ankhondo,+ Mwakwiya. Tiloleni tibwerere kwa inu.+   Mwagwedeza dziko lapansi, ndipo mwaling’amba.+ Tsekani ming’alu yake, pakuti lagwedezeka.+   Anthu anu mwawaonetsa zovuta.+ Mwatimwetsa vinyo ndipo tikuyenda dzandidzandi.+   Anthu okuopani mwawapatsa chizindikiro+ Kuti athawe uta mokhotakhota. [Seʹlah.]   Kuti okondedwa anu apulumutsidwe,+ Tipulumutseni ndi dzanja lanu lamanja ndi kutiyankha.+   Pokhala woyera, Mulungu walankhula kuti:+ “Ndidzakondwa ndi kupereka Sekemu ngati gawo la cholowa.+ Ndipo ndidzayezera anthu anga chigwa cha Sukoti.+   Giliyadi ndi wanga ndipo Manase ndi wanganso.+ Efuraimu ndi malo otetezeka a mtsogoleri amene ine ndamuika. Yuda ndi ndodo ya mtsogoleri wanga.+   Mowabu ndi beseni langa losambiramo.+ Ndidzaponyera Edomu nsapato zanga.+ Ndidzafuula mosangalala chifukwa chogonjetsa Filisitiya.”+   Ndani adzandibweretsa kumzinda wozunguliridwa ndi adani?+ Ndani adzanditsogolera mpaka kukafika ku Edomu?+ 10  Ndinu Mulungu amene mungatichititse kupambana! Koma onani tsopano mwatitaya,+ Ndipo inu Mulungu wathu, simukupita kunkhondo pamodzi ndi magulu athu ankhondo.+ 11  Tithandizeni kuti tichoke m’masautso,+ Pakuti chipulumutso chochokera kwa munthu wochokera kufumbi n’chopanda pake.+ 12  Ndi thandizo la Mulungu, tidzalandira mphamvu,+ Ndipo Mulungu adzapondereza adani athu.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Sl 16:Kamutu.