Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 6:1-10

Kwa wotsogolera nyimbo: Nyimboyi iimbidwe chapansipansi* ndi zoimbira za zingwe.+ Nyimbo ya Davide. 6  Inu Yehova, musandidzudzule mutakwiya.+ Musandiwongolere mutapsa mtima.+   Ndikomereni mtima, inu Yehova, chifukwa ndikulefuka.+ Ndichiritseni,+ inu Yehova, chifukwa mafupa anga agwedezeka.   Moyo wanga wasokonezeka kwambiri.+ Kodi inu Yehova, mudzadikira kufikira liti?+   Bwererani+ mudzapulumutse moyo wanga, inu Yehova.+ Ndipulumutseni chifukwa cha kukoma mtima kwanu kosatha.+   Pakuti akufa satchula za inu.+ Kodi ndani angatamande inu ali m’Manda?*+   Ndalefuka chifukwa cha kuusa moyo* kwanga.+ Usiku wonse ndimanyowetsa bedi langa.+ Ndimakhathamitsa bedi langa ndi misozi.+   Maso anga achita mdima chifukwa cha chisoni changa.+ Maso anga akalamba chifukwa cha anthu onse ondichitira zoipa.+   Ndichokereni pamaso panga inu nonse ochita zopweteka ena,+ Chifukwa Yehova adzamva ndithu mawu a kulira kwanga.+   Yehova adzamva ndithu pempho langa loti andikomere mtima.+ Yehova adzalandira pemphero langa.+ 10  Adani anga onse adzachita manyazi kwambiri+ ndipo adzasokonezeka. Adzabwerera, ndipo nthawi yomweyo adzachita manyazi.+

Mawu a M'munsi

N’kutheka kuti mawu amene tawamasulira kuti “chapansipansi” akutanthauza kuti anali kuimba nyimbo imeneyi motsitsa kapena mwabesi.
Onani Zakumapeto 5.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.