Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 58:1-11

Kwa wotsogolera nyimbo. “Musandiwononge.” Salimo la Davide. Mikitamu.* 58  Kodi mungalankhule bwanji za chilungamo mutakhala chete?+ Kodi mungaweruze molungama, inu ana a anthu?+   Ayi! Inu mukuchita zosalungama padziko lapansi mogwirizana ndi zimene mtima wanu ukufuna,+ Ndipo mukukonza njira zochitira chiwawa ndi manja anu.+   Oipa akhala opotoka maganizo kuyambira ali m’mimba.+ Iwo asochera kuyambira ali m’mimba, Ndipo amalankhula zabodza.+   Iwo ali ndi poizoni ngati wa njoka,+ Ndipo ndi ogontha ngati njoka ya mamba imene yatseka makutu ake,+   Imene singamve mawu a munthu wamatsenga,+ Ngakhale wina wanzeru ataimanga ndi mphamvu zamatsenga.+   Inu Mulungu, agululeni mano m’kamwa mwawo.+ Inu Yehova, thyolani nsagwada za mkango wamphamvu.   Asungunuke ndi kupita ngati madzi.+ Mulungu akunge uta woponyera mivi yake pamene adaniwo akugwa.+   Woipayo amayenda ngati nkhono imene ikusungunuka. Iwo sadzaona dzuwa ngati mwana wa mayi amene wapita padera.+   Miphika yanu isanayambe kumva kutentha kwa moto wa mitengo yaminga,+ Mulungu adzauluza ndi mphepo yamkuntho mitengo yaiwisi yaminga pamodzi ndi imene ikuyaka.+ 10  Wolungama adzasangalala chifukwa chakuti waona oipa akupatsidwa chilango.+ Adzasambitsa mapazi ake m’magazi a anthu oipa.+ 11  Ndipo mtundu wa anthu udzati:+ “Ndithudi wolungama adzalandira mphoto.+ Ndithudi pali Mulungu amene akuweruza dziko lapansi.”+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Sl 16:Kamutu.