Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 57:1-11

Kwa wotsogolera nyimbo. “Musandiwononge.” Salimo la Davide. Mikitamu.* Pa nthawi imene anathawa Sauli n’kukalowa m’phanga.+ 57  Ndikomereni mtima inu Mulungu, ndikomereni mtima,+ Pakuti ine ndathawira kwa inu.+ Ndipo ndathawira mumthunzi wa mapiko anu kufikira masoka atadutsa.+   Ndikufuulira Mulungu Wam’mwambamwamba,  Mulungu woona amene akuthetsa masoka amenewa kuti zinthu zindiyendere bwino.+   Adzatumiza thandizo kuchokera kumwamba ndi kundipulumutsa.+ Adzasokoneza wofuna kundiwakha ndi pakamwa pake.+ [Seʹlah.] Mulungu adzasonyeza kukoma mtima kwake kosatha ndi choonadi chake.+   Moyo wanga uli pakati pa mikango.+ Sindingachitire mwina koma kugona pakati pa ana a anthu, amene ali ngati nyama zoopsa zodya anthu, Amene mano awo ali ngati mikondo ndi mivi,+ Ndipo lilime lawo lili ngati lupanga lakuthwa.+   Inu Mulungu, kwezekani kupitirira kumwamba.+ Ulemerero wanu ukhale pamwamba pa dziko lonse lapansi.+   Iwo anditchera ukonde panjira yanga.+ Moyo wanga wagwidwa ndi chisoni.+ Andikumbira mbuna. Koma iwo agweramo.+ [Seʹlah.]   Mtima wanga wakhazikika, Inu Mulungu,+ Mtima wanga wakhazikika. Ndidzaimba nyimbo zokutamandani.+   Iwe mtima wanga, galamuka.+ Iwe choimbira cha zingwe, galamuka, ndi iwenso zeze.+ Ndidzadzuka m’bandakucha usanafike.   Ndidzakutamandani pakati pa mitundu ya anthu, inu Yehova.+ Ndidzaimba nyimbo zokutamandani pakati pa mitundu ya anthu.+ 10  Pakuti kukoma mtima kwanu kosatha n’kwakukulu ndipo kwafika kumwamba,+ Choonadi chanu chafika kuthambo.+ 11  Inu Mulungu, kwezekani kupitirira kumwamba.+ Ulemerero wanu ukhale pamwamba pa dziko lonse lapansi.

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Sl 16:Kamutu.