Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 56:1-13

Kwa wotsogolera nyimbo pa “Nkhunda Yosanena Kanthu” pakati pa okhala kutali. Salimo la Davide. Mikitamu.* Pa nthawi imene Afilisiti anamugwira ku Gati.+ 56  Ndikomereni mtima inu Mulungu wanga, chifukwa munthu wopanda pake akufuna kundiwakha ndi pakamwa pake.+ Akulimbana nane tsiku lonse ndi kundipondereza.+   Tsiku lonse adani anga akufuna kundiwakha ndi pakamwa pawo,+ Pakuti anthu ambiri akumenyana nane modzikuza.+   Ine ndidzadalira inu, tsiku lililonse limene ndingachite mantha.+   Popeza kuti ndine wogwirizana ndi Mulungu, ndidzatamanda mawu ake.+ Ine ndimadalira Mulungu, sindidzaopa.+ Kodi munthu angandichite chiyani?+   Tsiku lonse amasokoneza zolinga zanga. Nthawi zonse amaganiza zondichitira zoipa.+   Amandiukira ndi kundibisalira,+ Iwo nthawi zonse amaonetsetsa mmene ndikuyendera,+ Pamene akundidikirira kuti awononge moyo wanga.+   Atayeni chifukwa cha zochita zawo zoipa.+ Inu Mulungu, gwetsani mitundu ya anthu mu mkwiyo wanu.+   Inu mwalemba za kuthawathawa kwanga.+ Sungani misozi yanga m’thumba lanu lachikopa.+ Kodi misozi yanga sili m’buku lanu?+   Pa nthawi imeneyo adani anga adzabwerera pa tsiku limene ndidzaitana inu.+ Ndikudziwa bwino kuti Mulungu ali kumbali yanga.+ 10  Popeza kuti ndine wogwirizana ndi Mulungu,+ ndidzatamanda mawu ake. Popeza kuti ndine wogwirizana ndi Yehova, ndidzatamanda mawu ake.+ 11  Ine ndimadalira Mulungu. Sindidzaopa.+ Kodi munthu wochokera kufumbi angandichite chiyani?+ 12  Inu Mulungu, ine ndikuyenera kukwaniritsa malonjezo anga kwa inu.+ Ndidzapereka kwa inu nsembe zoyamikira.+ 13  Pakuti inu mwalanditsa moyo wanga ku imfa.+ Inu mwateteza phazi langa kuti lisapunthwe,+ Kuti ndiyendeyende pamaso pa Mulungu m’kuwala kumene kumaunikira anthu amoyo.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Sl 16:Kamutu.