Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 55:1-23

Kwa wotsogolera nyimbo: Nyimboyi iimbidwe ndi zipangizo za zingwe. Masikili.* Salimo la Davide. 55  Inu Mulungu, mvetserani pemphero langa.+ Musanyalanyaze pempho langa lakuti mundikomere mtima.+   Ndimvetsereni mwatcheru ndi kundiyankha.+ Mtima wanga suli m’malo chifukwa cha mavuto anga,+ Sindingachitire mwina koma kusonyeza nkhawa zanga,   Chifukwa cha zimene adani akunena, ndiponso chifukwa chakuti oipa andipanikiza.+ Pakuti akundikhuthulira mavuto,+ Ndipo mwaukali akundisungira chidani.+   Mtima wanga ukundipweteka kwambiri.+ Ndipo ndikuopa imfa.+   Ndagwidwa ndi mantha ndipo ndikunjenjemera.+ Inde ndikunthunthumira.   Ndipo ndikunena kuti: “Ndikanakhala ndi mapiko ngati njiwa!+ Ndikanauluka ndi kukakhala kwina.+   Ndikanathawira kutali.+ Ndikanapita kukakhala m’chipululu.+ [Seʹlah.]   Ndikanathawira kumalo opulumukirako, Kuthawa mphepo yamphamvu, ndithu kuthawa mphepo yamkuntho.”+   Inu Yehova, sokonezani anthu oipa, ndipo sokonezani zonena zawo,+ Pakuti ndaona ziwawa ndi mikangano mumzinda.+ 10  Usana ndi usiku amayenda pamwamba pa mpanda kuzungulira mzindawo.+ Ndipo mumzindawo muli zopweteka ndi masautso.+ 11  Mmenemo muli mavuto okhaokha. Ndipo kuponderezana ndi chinyengo sizinachoke kubwalo la mzindawo.+ 12  Pakuti amene ananditonza si mdani.+ Akanakhala mdani ndikanapirira. Amene anadzikweza pamaso panga si munthu wodana nane kwambiri.+ Akanakhala munthu wodana nane kwambiri ndikanabisala.+ 13  Koma ndiwe, munthu wofanana ndi ine,+ Munthu amene ndimam’dziwa bwino ndiponso mnzanga weniweni,+ 14  Chifukwa tinali mabwenzi apamtima.+ Tinali kuyenda limodzi ndi khwimbi la anthu kupita kunyumba ya Mulungu.+ 15  Chiwonongeko chiwagwere!+ Atsikire ku Manda ali amoyo.+ Pakuti kulikonse kumene apita, zinthu zoipa zimakhala mumtima mwawo.+ 16  Koma ine ndidzafuulira Mulungu.+ Ndipo Yehova adzandipulumutsa.+ 17  Usiku, m’mawa ndi masana ndimakhala ndi nkhawa ndipo ndimakhala ndikulira,+ Choncho Mulungu amamva mawu anga.+ 18  Iye adzandiwombola ndi kundikhazika pa mtendere, kundichotsa pankhondo,+ Pakuti khamu la anthu landiukira.+ 19  Mulungu amene wakhala pampando wachifumu kuyambira kalekale,+ Adzandimvera ndipo adzawayankha,+ [Seʹlah.] Anthu osafuna kusintha makhalidwe awo oipa,+ Ndiponso amene saopa Mulungu.+ 20  Iye watambasula dzanja lake kuukira anthu amene ali naye pa mtendere.+ Wanyoza pangano lake.+ 21  Mawu a pakamwa pake ndi osalala ngati mafuta a mkaka,+ Koma mtima wake umakonda ndewu.+ Mawu ake ndi osalala ngati mafuta,+ Koma ali ngati lupanga lakuthwa.+ 22  Umutulire Yehova nkhawa zako,+ Ndipo iye adzakuchirikiza.+ Sadzalola kuti wolungama agwedezeke.+ 23  Koma inu Mulungu, mudzatsitsira oipa kumanda.+ Ndipo anthu amene ali ndi mlandu wa magazi komanso anthu achinyengo, sadzakwanitsa kukhala ngakhale hafu ya moyo wawo.+ Koma ine ndidzakhulupirira inu.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Sl 32:Kamutu.