Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 54:1-7

Kwa wotsogolera nyimbo: Nyimboyi iimbidwe ndi zipangizo za zingwe. Masikili.* Salimo la Davide. Pa nthawi imene Zifi anabwera kudzauza Sauli kuti: “Kodi simukudziwa kuti Davide akubisala kwathu?”+ 54  Inu Mulungu, ndipulumutseni m’dzina lanu,+ Ndipo ndithandizeni ndi mphamvu zanu.+   Inu Mulungu, imvani pemphero langa.+ Tcherani khutu ku mawu ochokera m’kamwa mwanga.+   Pakuti pali anthu achilendo amene andiukira, Ndipo pali olamulira ankhanza amene akufuna moyo wanga.+ Sanaike Mulungu patsogolo pawo.+ [Seʹlah.]   Taonani! Mulungu ndiye mthandizi wanga.+ Yehova ali pakati pa anthu amene akuchirikiza moyo wanga.   Iye adzabwezera zoipa kwa adani anga.+ Achititseni kukhala chete chifukwa cha choonadi chanu.+   Ndidzapereka nsembe kwa inu mofunitsitsa.+ Inu Yehova, ndidzatamanda dzina lanu pakuti ndi labwino.+   Pakuti anandilanditsa pa mavuto anga onse,+ Ndipo diso langa laona adani anga atagonja.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Sl 32:Kamutu.