Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 53:1-6

Kwa wotsogolera nyimbo pa Mahalati.*+ Masikili.* Salimo la Davide. 53  Wopusa amanena mumtima mwake kuti:“Kulibe Yehova.”+Anthu oterewa amachita zoipa, ndipo amachita zinthu zonyansa zogwirizana ndi kupanda chilungamo kwawo.Palibe amene akuchita zabwino.+   Koma kuchokera kumwamba, Mulungu wayang’ana ana a anthu padziko lapansi,+Kuti aone ngati pali aliyense wozindikira, aliyense amene akufunafuna Yehova.   Onse abwerera, ndipo onsewo ndi achinyengo.Palibe aliyense amene akuchita zabwino,Palibiretu ndi mmodzi yemwe.   Kodi palibe aliyense wozindikira mwa anthu ochita zopweteka anzawowa,+Amene akudya anthu anga ngati chakudya?+Iwo sanaitane pa Yehova.+   Nthawi yomweyo anagwidwa ndi mantha aakulu,Ngakhale kuti panalibe chochititsa mantha.Pakuti Mulungu adzamwaza mafupa a aliyense womanga msasa kuti akuukireni.+Isiraeli adzawachititsa manyazi pakuti Yehova wawakana.   Haa! Zikanakhala bwino m’Ziyoni mukanapezeka chipulumutso cha Isiraeli.+Yehova akadzasonkhanitsa ndi kubwezeretsa anthu ake amene agwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,+Yakobo adzasangalale, Isiraeli adzakondwere.

Mawu a M'munsi

“Mahalati” ndi mawu achiheberi. N’kutheka kuti ndi mawu okhudzana ndi nyimbo, mwina okhudzana ndi luso la kaimbidwe.
Onani mawu a m’munsi pa Sl 32:Kamutu.