Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 52:1-9

Kwa wotsogolera nyimbo. Masikili.* Salimo la Davide, pa nthawi imene Doegi, Mwedomu, anapita kwa Sauli kukamuuza kuti Davide wapita kunyumba ya Ahimeleki.+ 52  N’chifukwa chiyani ukudzitukumula chifukwa cha zinthu zoipa, wamphamvu iwe?+ Kukoma mtima kosatha kwa Mulungu n’kokhalitsa.+   Lilime lako limakonza chiwembu, ndipo ndi lakuthwa ngati lezala,+ Limachita zachinyengo.+   Umakonda kwambiri zinthu zoipa kuposa zabwino,+ Umakonda kwambiri kulankhula chinyengo kuposa kulankhula chilungamo.+ [Seʹlah.]   Umakonda mawu onse owononga,+ Lilime lachinyengo iwe.+   Mulungu adzakupasula kosatha.+ Adzakugwetsa ndi kukukokera kunja kwa hema wako,+ Ndipo adzakuzula ndithu m’dziko la anthu amoyo.+ [Seʹlah.]   Olungama adzaona zimenezi ndi kuchita mantha,+ Ndipo adzamuseka.+   Munthu wamphamvu wotere sadalira Mulungu monga malo ake achitetezo,+ Koma amadalira kuchuluka kwa chuma chake,+ Ndipo chitetezo chake amachipeza m’mavuto amene iyeyo amawachititsa.+   Koma ine ndidzakhala ngati mtengo waukulu wa maolivi+ wa masamba obiriwira m’nyumba ya Mulungu. Ndidzakhulupirira kukoma mtima kosatha kwa Mulungu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+   Ndidzakutamandani mpaka kalekale, chifukwa cha zimene mwachita.+ Ndipo ndidzayembekezera dzina lanu pamaso pa okhulupirika anu, chifukwa ndi labwino.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Sl 32:Kamutu.