Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 50:1-23

Nyimbo ya Asafu.+ 50  Wamphamvuyo,+ Yehova, Mulungu,+ walankhula+ Ndipo akuitana dziko lapansi,+ Kuchokera kotulukira dzuwa mpaka kumene limalowera.+   Mulungu wawala ali ku Ziyoni,+ mzinda wokongola kwambiri.+   Mulungu wathu adzabwera ndipo sadzakhala chete.+ Pamaso pake pali moto wonyeketsa,+ Ndipo pamalo onse omuzungulira pali mkuntho wamphamvu.+   Akuitana kumwamba ndi dziko lapansi+ Kuti apereke chiweruzo kwa anthu ake. Iye akuti:+   “Sonkhanitsani okhulupirika anga kwa ine,+ Amene achita pangano mwa kupereka nsembe.”+   Ndipo kumwamba kukunena za chilungamo chake,+ Pakuti Mulungu ndiye Woweruza.+ [Seʹlah.]   “Ndimvereni anthu anga, ndipo ine ndilankhula,+ Inu Aisiraeli, ine ndipereka umboni wotsutsana nanu.+ Ine ndine Mulungu, Mulungu wanu.+   Sindikukudzudzulani chifukwa cha nsembe zanu,+ Kapena chifukwa cha nsembe zanu zopsereza zathunthu zimene mumapereka kwa ine nthawi zonse.+   Sindidzatenga ng’ombe yamphongo m’nyumba yanu,+ Kapena mbuzi yamphongo m’makola anu. 10  Pakuti nyama iliyonse yakutchire ndi yanga,+ Ndiponso nyama zopezeka m’mapiri 1,000.+ 11  Ndikudziwa bwino zolengedwa zonse zouluka za m’mapiri,+ Ndipo magulu a nyama zakutchire ndi anga.+ 12  Ngakhale nditakhala ndi njala, sindingakuuze, Pakuti dziko lonse+ ndiponso zonse za mmenemo ndi zanga.+ 13  Kodi ndiyenera kudya nyama ya ng’ombe zamphongo zonenepa,+ Kapena kumwa magazi a mbuzi zamphongo?+ 14  Pereka nsembe zoyamikira kwa Mulungu,+ Ndipo pereka kwa Wam’mwambamwamba zimene walonjeza.+ 15  Pa tsiku la nsautso undiitane.+ Ine ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza.”+ 16  Koma Mulungu adzauza woipa kuti:+ “Ndani wakupatsa udindo wofotokoza malangizo anga,+ Ndi wolankhula za pangano langa?+ 17  Iwe umadana ndi malangizo,*+ Ndipo umaponya mawu anga kunkhongo.+ 18  Nthawi zonse ukaona wakuba unali kusangalala naye.+ Ndipo unali kugwirizana ndi anthu achigololo.+ 19  Walekerera pakamwa pako kulankhula zinthu zoipa,+ Ndipo ukugwiritsa ntchito lilime lako kulankhula zachinyengo.+ 20  Umakhala pansi ndi kunenera m’bale wako zinthu zoipa,+ Umapezera zifukwa mwana wamwamuna wa mayi ako.+ 21  Wachita zinthu zonsezi, koma ine ndinakhala chete.+ Unali kuganiza kuti ine ndikhala ngati iwe.+ Ine ndidzakudzudzula,+ ndipo ndidzaika machimo ako onse poyera iwe ukuona.+ 22  Zindikirani zimenezi, anthu oiwala Mulungu inu,+ Kuti ndisakukhadzulekhadzuleni popanda aliyense wokupulumutsani.+ 23  Amene akupereka nsembe yoyamikira kwa ine ndi amene akundilemekeza.+ Ndipo amene akuyenda panjirayo motsimikiza, Ndidzamuonetsa chipulumutso changa.”+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.