Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 49:1-20

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.+ 49  Mvetserani izi, anthu nonsenu. Tcherani khutu inu nonse a m’nthawi* ino,+   Inu mtundu wa anthu ndiponso inu ana a anthu, Inu olemera pamodzi ndi inu osauka.+   Pakamwa panga padzalankhula zinthu zanzeru,+ Ndipo zosinkhasinkha za mtima wanga zidzakhala zinthu zakuya.+   Ndidzatchera khutu kuti ndimvetsere mwambi.+ Poimba zeze ndidzamasulira mawu anga ophiphiritsa.+   Ndichitirenji mantha m’masiku oipa,+ Pamene zolakwa za ofuna kundigwetsa zandizinga?+   Anthu amene akukhulupirira chuma chawo,+ Amene akudzitamandira chifukwa cha kuchuluka kwa chuma chawo,+   Palibe ngakhale mmodzi wa iwo amene angathe kuwombola m’bale wake,+ Kapena kumuperekera dipo* kwa Mulungu,   (Ndipo malipiro owombolera moyo wawo ndi amtengo wapatali,+ Moti munthu sangathe kuwapereka mpaka kalekale)   Kuti akhale ndi moyo mpaka muyaya osaona dzenje la manda.+ 10  Pakuti amaona kuti ngakhale anthu anzeru amafa,+ Wopusa ndi wopanda nzeru, onsewo amawonongeka,+ Ndipo chuma chawo amasiyira anthu ena.+ 11  Zokhumba za mtima wawo n’zakuti nyumba zawo zikhalebe mpaka kalekale,+ Mahema awo akhalebe ku mibadwomibadwo.+ Malo awo amawatcha mayina awo.+ 12  Komabe munthu wochokera kufumbi, ngakhale atakhala wolemekezeka, sangakhale ndi moyo mpaka kalekale.+ Iye amangofanana ndi nyama zimene zaphedwa.+ 13  Umu ndi mmene zimakhalira ndi zitsiru,+ Komanso amene amazitsanzira, omwe amasangalala ndi mawu awo odzitukumula.  [Seʹlah.] 14  Awatsogolera ku Manda ngati nkhosa zopita kokaphedwa.+ Imfa idzakhala m’busa wawo.+ Ndipo m’mawa anthu owongoka mtima adzawalamulira.+ Matupi awo adzawonongeka.+ Aliyense wa iwo malo ake okhala ndi ku Manda, osati malo okwezeka.+ 15  Koma Mulungu adzawombola moyo wanga ku Manda,+ Pakuti adzandilandira. [Seʹlah.] 16  Musachite mantha chifukwa chakuti munthu wina akupeza chuma,+ Kapena chifukwa chakuti ulemerero wa nyumba yake ukuwonjezeka,+ 17  Pakuti pa imfa yake sangatenge kena kalikonse.+ Ulemerero wake sudzapita naye pamodzi.+ 18  Pakuti pamene anali moyo anali kutamanda moyo wake,+ (Ndipo anthu adzakutamanda chifukwa chakuti walemera)+ 19  Moyo wake udzafanana ndi wa m’badwo wa makolo ake.+ Ndipo iwo sadzaonanso kuwala.+ 20  Munthu, ngakhale atakhala wolemekezeka, koma ngati ali wosazindikira,+ Amangofanana ndi nyama zimene zaphedwa.+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.