Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Masalimo 48:1-14

Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.+ 48  Yehova ndi wamkulu ndi woyenera kutamandidwa kwambiri,+ Mumzinda wa Mulungu wathu,+ m’phiri lake loyera.+   Phiri la Ziyoni limene lili m’dera lakutali la kumpoto,+ Ndi lokongola chifukwa lili pamalo okwezeka ndi osangalatsa padziko lonse lapansi,+ Mudzi wa Mfumu Yaikulu.+   Munsanja zokhalamo za m’mudzimo, Mulungu wadziwika kuti ndi malo okwezeka ndiponso achitetezo.+   Taonani! Mafumu anakumana atapangana,+ Koma anangodutsa.+   Iwo anaona ndipo anadabwa. Anasokonezeka, moti anathawa mopanikizika kwambiri.+   Kumeneko iwo anayamba kunjenjemera,+ Anamva zopweteka ngati za mkazi amene akubereka.+   Pogwiritsa ntchito mphepo yamphamvu ya kum’mawa, munaswa zombo za ku Tarisi.+   Ife taona zimene Mulungu anachita monga mmene tinamvera,+ Mumzinda wa Yehova wa makamu, mumzinda wa Mulungu wathu.+ Mulungu adzakhazikitsa mzindawo mpaka kalekale.+ [Se′lah.]   Inu Mulungu, ife talingalira mozama za kukoma mtima kwanu kosatha,+ Tili mkati mwa kachisi wanu.+ 10  Inu Mulungu, mofanana ndi dzina lanu,+ kukutamandani Kwafika kumalire a dziko lapansi. Dzanja lanu lamanja ladzaza ndi chilungamo.+ 11  Phiri la Ziyoni+ likondwere, Midzi yozungulira Yuda isangalale+ chifukwa cha zigamulo zanu.+ 12  Gubani mozungulira Ziyoni, anthu inu, ndipo yendayendani mmenemo,+ Werengani nsanja zake.+ 13  Ganizirani mofatsa za khoma lake lolimba.+ Yenderani nsanja zake zokhalamo, Kuti mudzasimbire m’badwo wam’tsogolo.+ 14  Pakuti Mulungu uyu ndi Mulungu wathu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+ Iye adzatitsogolera kufikira imfa yathu.+

Mawu a M'munsi