Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 47:1-9

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora. 47  Ombani m’manja anthu nonsenu.Fuulirani Mulungu mokondwera chifukwa chakuti wapambana.   Pakuti Yehova, Wam’mwambamwamba, ndi wochititsa mantha,Ndiye Mfumu yaikulu padziko lonse lapansi.+   Iye adzagonjetsa mitundu ya anthu ndi kuiika pansi pathu.+Adzagonjetsa anthu a mitundu ina ndi kuwaika pansi pa mapazi athu.   Adzatisankhira cholowa,Chimene Yakobo, amene amamukonda, anakondwera nacho. [Seʹlah.]   Mulungu wakwera kumalo ake, anthu akufuula mokondwera,+Yehova wakwera kumalo ake, anthu akuliza lipenga la nyanga ya nkhosa.   Imbani nyimbo zotamanda Mulungu, imbani nyimbo zotamanda.Imbani nyimbo zotamanda Mfumu yathu, imbani nyimbo zotamanda.   Pakuti Mulungu ndi Mfumu ya dziko lonse lapansi.+Imbani nyimbo zotamanda ndi kuchita zinthu mozindikira.+   Mulungu wakhala mfumu ya mitundu ya anthu.Mulungu wakhala pampando wake wachifumu wopatulika.+   Atsogoleri a mitundu ya anthu asonkhana.+Asonkhana pamodzi ndi anthu a Mulungu wa Abulahamu.+Pakuti anthu onse omwe ali ngati zishango* za dziko lapansi ndi a Mulungu.+Iye wakwera pamalo okwezeka kwambiri.+

Mawu a M'munsi

N’kutheka kuti mawu akuti “zishango” akunena olamulira kapena oteteza anthu.