Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 46:1-11

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la ana a Kora+ mogwirizana ndi kaimbidwe ka Atsikana. 46  Mulungu ndiye pothawira pathu ndi mphamvu yathu,+ Thandizo lopezeka mosavuta pa nthawi ya masautso.+   N’chifukwa chake sitidzaopa, ngakhale dziko lapansi litasintha,+ Ndiponso ngakhale mapiri atagwedezeka ndi kumira m’nyanja yaikulu.+   Ngakhale madzi a m’nyanjayo atawinduka ndi kuchita thovu,+ Ndiponso ngakhale mapiri atagwedezeka chifukwa cha phokoso la nyanja yaikuluyo.+ [Seʹlah.]   Pali mtsinje womwe nthambi zake zimachititsa anthu a mumzinda wa Mulungu kukondwera,+ Chihema chachikulu chopatulika koposa cha Wam’mwambamwamba.+   Mulungu ali pakati pa mzinda.+ Mzindawo sudzagwedezeka.+ Mulungu adzauthandiza m’bandakucha.+   Mitundu ya anthu inachita phokoso,+ maufumu anagwedezeka. Iye anatulutsa mawu ndipo dziko lapansi linasungunuka.+   Yehova wa makamu ali ndi ife.+ Mulungu wa Yakobo ndiye malo athu okwezeka ndiponso achitetezo.+ [Seʹlah.]   Bwerani anthu inu, onani ntchito za Yehova,+ Onani mmene wakhazikitsira zinthu zodabwitsa padziko lapansi.+   Akuletsa nkhondo mpaka kumalekezero a dziko lapansi.+ Wathyola uta ndi kuduladula mkondo.+ Ndipo watentha magaleta pamoto.+ 10  “Gonjerani anthu inu, ndipo dziwani kuti ine ndine Mulungu.+ Ndidzakwezedwa pakati pa anthu a mitundu ina,+ Ndidzakwezedwa padziko lapansi.”+ 11  Yehova wa makamu ali ndi ife.+ Mulungu wa Yakobo ndiye malo athu okwezeka ndiponso achitetezo.+ [Seʹlah.]

Mawu a M'munsi