Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Masalimo 45:1-17

Kwa wotsogolera nyimbo pa Maluwa.* Salimo la ana a Kora. Masikili.* Nyimbo yonena za akazi okondedwa. 45  Mtima wanga wagalamuka chifukwa cha nkhani yosangalatsa.+ Ine ndikuti: “Nyimbo yangayi ikunena za mfumu.”+ Lilime langa likhale ngati cholembera+ cha wokopera malemba waluso.+   Ndiwedi wokongola kwambiri kuposa ana a anthu.+ Mawu otuluka m’kamwa mwako ndi osangalatsadi.+ N’chifukwa chake Mulungu adzakupatsa madalitso mpaka kalekale.+   Mangirira lupanga lako+ m’chiuno mwako wamphamvu iwe,+ Limodzi ndi ulemu ndiponso ulemerero wako.+   Ndipo upambane mu ulemerero wako.+ Kwera pahatchi yako chifukwa cha choonadi, kudzichepetsa ndi chilungamo,+ Ndipo dzanja lako lamanja lidzakulangiza mu zinthu zochititsa mantha.+   Mivi yako yakuthwa idzalasa mitima ya adani a mfumu,+ Mitundu ya anthu idzagwa pamapazi ako.+   Mulungu ndiye mpando wako wachifumu mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+ Ndodo yako yachifumu ndiyo ndodo yachilungamo.+   Umakonda chilungamo+ ndipo umadana ndi zoipa.+ N’chifukwa chake Mulungu, Mulungu wako,+ wakudzoza+ ndi mafuta achikondwerero chachikulu+ kuposa cha mafumu ena.+   Zovala zako zonse ndi zonunkhira mafuta a mule, aloye ndi kasiya.*+ Umasangalala ndi nyimbo zoimbidwa ndi zipangizo za zingwe, kuchokera m’chinyumba chachikulu cha mfumu, chokongoletsedwa ndi minyanga ya njovu.+   Ana aakazi+ a mafumu ali m’gulu la akazi ako okondedwa. Mkazi wamkulu wa mfumu+ waima kudzanja lako lamanja atavala zovala zagolide wa ku Ofiri.+ 10  Iwe mwana wanga wamkazi, mvetsera ndipo ona ndi kutchera khutu. Uiwale anthu ako ndi nyumba ya bambo ako.+ 11  Mfumu idzalakalaka kukongola kwako,+ Pakuti ndiyo mbuye wako,+ Choncho iweramire.+ 12  Mwana wamkazi wa ku Turo alinso komweko ndi mphatso,+ Olemera pakati pa anthu adzakhazika pansi mtima wako.+ 13  Mwana wamkazi wa mfumu ali pa ulemerero waukulu m’nyumba ya mfumu.+ Zovala zake ndi zagolide. 14  Adzamubweretsa kwa mfumu atavala chovala choluka.+ Anamwali anzake omuperekeza akubwera nawo kwa iwe.+ 15  Adzawabweretsa akusangalala ndi kukondwera. Ndipo adzalowa m’nyumba ya mfumu. 16  Ana anu adzatenga+ malo a makolo anu,+ Ndipo mudzawaika kukhala akalonga padziko lonse lapansi.+ 17  Ndidzatchula dzina lanu m’mibadwo yonse yam’tsogolo.+ N’chifukwa chake mitundu ya anthu idzakutamandani mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.

Mawu a M'munsi

N’kutheka kuti “Maluwa” chinali chipangizo choimbira cha zingwe 6.
Onani mawu a m’munsi pa Sl 32:Kamutu.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.