Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 44:1-26

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la ana a Kora. Masikili.* 44  Inu Mulungu, ife tamva ndi makutu athu,Makolo athu anatifotokozeraNtchito zimene inu munachita m’masiku awo,+M’masiku akale.   Munapitikitsa anthu a mitundu ina ndi dzanja lanu,Ndipo m’malo mwawo munakhazikitsa anthu anu.Munagonjetsa mitundu ya anthu ndi kuipitikitsa.   Pakuti iwo sanatenge dzikolo chifukwa cha lupanga lawo,Ndipo si mkono wawo umene unawabweretsera chipulumutso.Koma chinabwera ndi dzanja lanu lamanja,+ mkono wanu ndi kuwala kwa nkhope yanu,Chifukwa munakondwera nawo.   Inu Mulungu, ndinu Mfumu yanga.+Lamulani kuti Yakobo alandire chipulumutso chachikulu.+   Ndi thandizo lanu tidzakankha adani athu.+M’dzina lanu tidzapondereza amene akutiukira.+   Pakuti sindinadalire uta wanga,+Ndipo si lupanga langa limene linandipulumutsa.   Ndinu amene munatipulumutsa kwa adani athu,+Ndipo munanyazitsa anthu amene amadana nafe kwambiri.+   Tidzayamika Mulungu nthawi zonse,+Tidzatamanda dzina lanu mpaka kalekale.+ [Seʹlah.]   Koma tsopano mwatitaya ndi kutichititsa manyazi,+Simukuyenda ndi magulu athu ankhondo.+ 10  Mwachititsa kuti tithawe pamaso pa adani athu,Ndipo anthu odana nafe kwambiri afunkha zinthu zathu.+ 11  Mwatipereka kwa adani athu kuti atidye ngati nkhosa,+Ndipo mwatimwaza pakati pa anthu a mitundu ina.+ 12  Mwagulitsa anthu anu pa mtengo wotsika kwambiri,Ndipo simunapeze phindu ndi mtengo wawo. 13  Mwatisandutsa chitonzo kwa anthu oyandikana nafe,+Mwatisandutsa chinthu chonyozeka ndi choseketsa kwa onse otizungulira.+ 14  Mwatisandutsa mwambi pakati pa anthu a mitundu ina,Mwatisandutsa anthu amene anthu a mitundu inawo akuwapukusira mitu.+ 15  Zondichititsa manyazi zili pamaso panga tsiku lonse,Ndipo manyazi aphimba nkhope yanga,+ 16  Chifukwa cha mawu a munthu wonditonza ndi wolankhula zachipongwe,Ndiponso chifukwa cha mdani wanga ndi wofuna kundibwezera choipa.+ 17  Zonsezi ndi zimene zatigwera, koma sitinakuiwaleni,Sitinachite mwachinyengo ndi pangano lanu. 18  Mitima yathu sinakhale yosakhulupirika n’kuchoka panjira yanu,+Ndipo mapazi athu sanapatuke panjira yanu.+ 19  Pakuti inu mwatiphwanya kumalo amene mimbulu imasonkhana,+Mwatiphimba ndi mdima wandiweyani.+ 20  Ngati tikanaiwala dzina la Mulungu wathu,Kapena kupemphera kwa mulungu wachilendo titakweza manja athu, 21  Kodi Mulungu sakanafufuza zimenezi?+Pakuti iye amadziwa zinsinsi za mumtima.+ 22  Koma chifukwa cha inu, tikuphedwa nthawi zonse.Takhala ngati nkhosa zokaphedwa.+ 23  Nyamukani. N’chifukwa chiyani mukugonabe, inu Yehova?+Dzukani. Musatitaye kwamuyaya.+ 24  N’chifukwa chiyani mukubisabe nkhope yanu?N’chifukwa chiyani mukuiwala masautso athu ndi kuponderezedwa kwathu?+ 25  Pakuti miyoyo yathu yasautsika.+Mimba zathu zili thasa! padothi. 26  Nyamukani kuti mutithandize+Tiwomboleni chifukwa cha kukoma mtima kwanu kosatha.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Sl 32:Kamutu.