Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 43:1-5

43  Ndiweruzeni+ inu Mulungu, Weruzani mlandu wanga+ motsutsana ndi mtundu wosakhulupirika. Ndipulumutseni kwa munthu wachinyengo ndi wochita zosalungama.+   Pakuti inu ndinu Mulungu wanga, ndinu malo anga achitetezo.+ N’chifukwa chiyani mwanditaya? Ndikuyenderanji wachisoni chifukwa choponderezedwa ndi mdani wanga?+   Tumizani kuwala kwanu ndi choonadi chanu.+ Zimenezi zinditsogolere.+ Zindifikitse kuphiri lanu lopatulika ndi kuchihema chanu chachikulu.+   Ndidzapita paguwa lansembe la Mulungu,+ Kwa Mulungu amene amandikondweretsa ndi kundisangalatsa.+ Ndipo ndidzakutamandani ndi zeze, inu Mulungu, Mulungu wanga.+   N’chifukwa chiyani ukutaya mtima, moyo wangawe?+ Ndipo n’chifukwa chiyani ukusautsika mkati mwanga? Yembekezera Mulungu,+ Ndipo ndidzamutamanda pakuti iye ndiye mpulumutsi wanga wamkulu ndi Mulungu wanga.+

Mawu a M'munsi