Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 42:1-11

Kwa wotsogolera nyimbo. Masikili* ya ana a Kora.+ 42  Monga mmene mbawala yaikazi imalakalakira mitsinje ya madzi, Moyo wanganso ukulakalaka inu Mulungu wanga.+   Moyo wanga ukulakalaka Mulungu,+ ukulakalaka Mulungu wamoyo.+ Ndidzapita liti kunyumba ya Mulungu kukaonekera pamaso pake?+   Misozi yanga yasanduka chakudya changa usana ndi usiku,+ Pamene anthu akundifunsa tsiku lonse kuti: “Mulungu wako ali kuti?”+   Ndidzakumbukira zinthu zakale ndipo moyo wanga udzavutika pokumbukira zimenezo.+ Pakuti ndinali kuyenda ndi khwimbi la anthu, Ndinali kuyenda pang’onopang’ono patsogolo pawo kupita kunyumba ya Mulungu,+ Tinali kufuula mosangalala ndi kuyamika Mulungu.+ Khamu la anthu okondwerera madyerero linali kunditsatira.+   N’chifukwa chiyani ukutaya mtima, moyo wangawe?+ Ndipo n’chifukwa chiyani ukusautsika mkati mwanga?+ Yembekezera Mulungu,+ Ndipo ndidzamutamanda pakuti iye ndiye mpulumutsi wanga wamkulu.+   Inu Mulungu wanga, ine ndataya mtima.+ N’chifukwa chake ndakumbukira inu,+ Pamene ndili m’dziko la Yorodano ndi m’mapiri a Herimoni,+ Pamene ndili m’phiri laling’ono.+   Madzi akuya akufuulira madzi akuya, Kudzera mu mkokomo wa madzi otumphuka. Mafunde anu onse amphamvu,+ Andimiza.+   Masana Yehova adzalamula kukoma mtima kwake kosatha kuti kufike pa ine,+ Ndipo usiku ndidzaimba za iye.+ Ndidzapemphera kwa Mulungu wondipatsa moyo.+   Ndidzauza Mulungu, thanthwe langa kuti:+ “N’chifukwa chiyani mwandiiwala?+ Ndikuyenderanji wachisoni chifukwa choponderezedwa ndi mdani wanga?”+ 10  Odana nane akunditonza kwambiri moti zikungokhala ngati mafupa anga aphwanyidwa,+ Pakuti anthu akundifunsa tsiku lonse kuti: “Mulungu wako ali kuti?”+ 11  N’chifukwa chiyani ukutaya mtima, moyo wangawe?+ Ndipo n’chifukwa chiyani ukusautsika mkati mwanga?+ Yembekezera Mulungu,+ Ndipo ndidzamutamanda pakuti iye ndiye mpulumutsi wanga wamkulu ndiponso ndiye Mulungu wanga.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Sl 32:Kamutu.