Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 41:1-13

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide. 41  Wodala ndi munthu amene amachita zinthu moganizira munthu wonyozeka.+ Pa tsiku la tsoka, Yehova adzamupulumutsa.+   Yehova adzamuteteza ndi kumusunga ali wamoyo.+ Adzatchedwa wodala padziko lapansi.+ Ndipo Mulungu sangamupereke kwa adani ake.+   Yehova adzachirikiza  wonyozekayo pamene  akudwala pabedi lake.+ Mudzamusamalira bwino kwambiri pamene akudwala.+   Koma ine ndinati: “Inu Yehova, ndikomereni mtima.+ Ndichiritseni, pakuti ndakuchimwirani.”+   Adani anga amanena zoipa zokhazokha za ine kuti:+ “Kodi ameneyu afa liti kuti dzina lake lifafanizike?”   Wina akabwera kudzandiona, amalankhula zabodza kuchokera mumtima mwake.+ Amasonkhanitsa nkhani zoipa. Akatero amachoka, ndipo kunjako amauza ena zabodza zokhudza ine.+   Mogwirizana, onse amene amadana nane amanong’onezana kuti andiukire.+ Amandikonzera chiwembu kuti andichitire zinthu zoipa. Iwo amati:+   “Amutsanulira tsoka.*+ Tsopano popeza iye wagona, sadzukanso.”+   Koma munthu amene ndinali kukhala naye mwamtendere, amene ndinali kumukhulupirira,+ Munthu amene anali kudya chakudya changa,+ wakweza chidendene chake kundiukira.+ 10  Koma inu Yehova, ndikomereni mtima ndi kundidzutsa,+ Kuti ndiwabwezere.+ 11  Mukatero ndidziwa kuti mwasangalala nane, Chifukwa mdani wanga sadzafuula mosangalala kuti wandipambana.+ 12  Koma ine mwandichirikiza chifukwa cha mtima wanga wosagawanika,+ Ndipo mudzandiika pamaso panu mpaka kalekale.+ 13  Adalitsike Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ Kuyambira kalekale mpaka kalekale.+ Ame! Ame!*+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “chinthu chopanda pake.”
Kapena kuti “Zikhale momwemo! Zikhale momwemo!”