Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 40:1-17

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide. 40  Ndinayembekezera Yehova ndi mtima wonse,+ Choncho iye anatchera khutu kwa ine ndipo anamva kufuula kwanga kopempha thandizo.+   Iye ananditulutsanso m’dzenje la madzi a mkokomo,+ Ananditulutsa m’chithaphwi cha matope.+ Kenako anapondetsa phazi langa pathanthwe.+ Anandiyendetsa panthaka yolimba.+   Komanso anaika mawu a nyimbo yatsopano m’kamwa mwanga, Nyimbo yotamanda Mulungu wathu.+ Ambiri adzaona zimenezi ndipo adzachita mantha,+ Iwo adzakhulupirira Yehova.+   Wodala ndi munthu wamphamvu amene amakhulupirira Yehova,+ Munthu amene sanacheukire anthu otsutsa, Kapena anthu amene anapatukira m’njira za mabodza.+   Inu Yehova Mulungu wanga, mwatichitira zinthu zambiri zodabwitsa,+ Ndipo mumatiganizira.+ Palibe angafanane ndi inu.+ Ndikafuna kulankhula ndi kunena za  zodabwitsazo, Zimachuluka kwambiri moti sindingathe kuzifotokoza.+   Nsembe ndiponso zopereka, simunasangalale nazo.+ Inu munatsegula makutu anga.+ Simunapemphe nsembe yopsereza ndi nsembe yamachimo.+   Chifukwa cha zimenezo ndinati: “Ine ndabwera,+ Pakuti mumpukutu munalembedwa za ine.+   Ndimakondwera ndi kuchita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga,+ Ndipo chilamulo chanu chili mumtima mwanga.+   Ndanena za uthenga wabwino wachilungamo mumpingo waukulu.+ Onani! Sindinatseke pakamwa panga.+ Inu Yehova, mukudziwa bwino zimenezi.+ 10  Chilungamo chanu sindinachibise mumtima mwanga.+ Ndinalengeza za kukhulupirika kwanu ndi chipulumutso chanu.+ Sindinabise kukoma mtima kwanu kosatha ndi choonadi chanu mumpingo waukulu.”+ 11  Inu Yehova, musasiye kundimvera chisoni.+ Kukoma mtima kwanu kosatha komanso choonadi chanu zinditeteze nthawi zonse.+ 12  Pakuti masoka anandizungulira moti sindinathe kuwawerenga.+ Zolakwa zanga zochuluka zinandifikira modzidzimutsa moti sindinathe kuziona mmene zinachulukira.+ Zinachuluka kwambiri kuposa tsitsi la kumutu kwanga,+ Ndipo ndinataya mtima.+ 13  Khalani wofunitsitsa kundilanditsa, inu Yehova.+ Inu Yehova, fulumirani kundithandiza.+ 14  Onse amene akufunafuna moyo wanga kuti aufafanize+ Achite manyazi ndi kuthedwa nzeru.+ Amene akukondwera ndi tsoka langa abwerere ndipo anyazitsidwe.+ 15  Onse amene akunena kuti: “Eyaa! Eyaa!”+ Ayang’anitsitse modabwa chifukwa cha manyazi awo.+ 16  Onse amene akufunafuna inu,+ Akondwere ndi kusangalala mwa inu.+ Onse amene amakonda chipulumutso chanu,+ Nthawi zonse azinena kuti: “Yehova alemekezeke.”+ 17  Koma ine ndasautsika ndipo ndasauka.+ Yehova amandiwerengera.+ Inu ndinu thandizo langa ndi Wopereka chipulumutso kwa ine.+ Inu Mulungu wanga musachedwe.+

Mawu a M'munsi