Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Masalimo 4:1-8

Kwa wotsogolera nyimbo: Nyimboyi iimbidwe ndi zipangizo za zingwe.+ Nyimbo ya Davide. 4  Ndikaitana, mundiyankhe inu Mulungu wanga wolungama.+ M’masautso anga mundiimiritse pamalo otakasuka. Mundikomere mtima+ ndipo imvani pemphero langa.   Inu ana a anthu, kodi mudzandinyoza chifukwa cha ulemerero wanga+ kufikira liti? Mudzakonda zinthu zopanda pake kufikira liti? Mudzafunafuna nkhani yoti mundinamizire kufikira liti? [Se′lah.]   Choncho dziwani kuti Yehova adzapatula wokhulupirika wake.+ Yehova adzamva ndikaitana.+   Ngati mwakwiya, musachimwe.+ Lankhulani mumtima mwanu, muli pabedi panu,+ ndipo mukhale chete. [Se′lah.]   Perekani nsembe zachilungamo,+ Ndipo khulupirirani Yehova.+   Pali ambiri amene akunena kuti: “Ndani adzationetsa zinthu zabwino?” Inu Yehova, tiunikeni ndi kuwala kwa nkhope yanu.+   Mudzasangalatsadi mtima wanga,+ Kuposanso mmene iwo amasangalalira, mbewu ndi vinyo wawo watsopano zikachuluka.+   Ndidzagona pansi ndi kupeza tulo mu mtendere,+ Pakuti inu nokha Yehova mumandichititsa kukhala wotetezeka.+

Mawu a M'munsi