Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 38:1-22

Nyimbo ya Davide ya chikumbutso. 38  Inu Yehova, musandidzudzule mutakwiya,+ Kapena kundilanga mutapsa mtima.+   Pakuti mivi yanu yandilasa kwambiri,+ Ndipo dzanja lanu likundilemera.+   Palibe pabwino m’thupi langa chifukwa cha chidzudzulo chanu.+ Ndipo m’mafupa anga mulibe mtendere chifukwa cha tchimo langa.+   Pakuti zolakwa zanga zakwera kupitirira mutu wanga.+ Zandilemera kwambiri ngati katundu wolemera.+   Zilonda zanga zanunkha ndi kunyeka, Chifukwa cha kupusa kwanga.+   Ndasokonezeka ndipo ndawerama kwambiri chifukwa cha chisoni changa.+ Ndayenda uku ndi uku tsiku lonse ndili wachisoni.+   M’chiuno mwanga mukutentha kwambiri, Ndipo palibe paliponse pabwino m’thupi langa.+   Ndalefuka ndipo ndaponderezeka kwambiri. Ndikulira mofuula chifukwa cha kuvutika kwa mtima wanga.+   Inu Yehova, zokhumba zanga zonse zili pamaso panu, Kudandaula kwanga sikunabisike kwa inu.+ 10  Mtima wanga ukugunda kwambiri, ndipo mphamvu zanga zatha, Maso anga achita mdima.+ 11  Anthu amene anali kundikonda ndiponso anzanga aima patali chifukwa cha kuvutika kwanga,+ Ndipo mabwenzi anga apamtima anditalikira.+ 12  Anthu amene akufuna kundiwononga anditchera misampha,+ Amene akufuna kundivulaza akulankhula motsutsana nane,+ Ndipo amakhala akukonza zachinyengo tsiku lonse.+ 13  Koma ine ndakhala ngati munthu wogontha, sindikumvetsera,+ Ndakhala ngati munthu wosalankhula, sindikutsegula pakamwa.+ 14  Ndakhala ngati munthu wosamva, Sindikulankhula zotsutsana nawo. 15  Pakuti ine ndikuyembekezera inu Yehova.+ Inu Yehova Mulungu wanga, mudzandiyankha.+ 16  Ine ndinati: “Ngati simundiyankha adani anga adzasangalala chifukwa cha kusautsika kwanga.+ Phazi langa likaterereka,+ iwo adzadzikweza pamaso panga.”+ 17  Ndinali pafupi kupunthwa,+ Ndipo ndinali kumva ululu nthawi zonse.+ 18  Pakuti ndinali kulankhula za cholakwa changa.+ Ndipo ndinali kudera nkhawa za tchimo langa.+ 19  Adani anga anali amphamvu kwambiri,+ Ndipo odana nane popanda chifukwa anachuluka.+ 20  Iwo anali kundibwezera choipa m’malo mwa chabwino,+ Ndikamayesetsa kuchita chabwino anali kunditsutsa.+ 21  Inu Yehova, musandisiye. Inu Mulungu wanga, musakhale kutali ndi ine.+ 22  Fulumirani kundithandiza,+ Inu Yehova, chipulumutso changa.+

Mawu a M'munsi