Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Masalimo 37:1-40

Salimo la Davide. א [ʼA′leph] 37  Usapse mtima chifukwa cha anthu ochita zoipa.+ Usakhumbe kukhala ngati anthu ochita zosalungama.+   Pakuti adzafota mwamsanga ngati udzu,+ Adzanyala ngati msipu watsopano wobiriwira.+ ב [Behth]   Khulupirira Yehova ndipo chita zabwino.+ Khala padziko lapansi, ndipo khala wokhulupirika m’zochita zako zonse.+   Komanso sangalala mwa Yehova,+ Ndipo adzakupatsa zokhumba za mtima wako.+ ג [Gi′mel]   Lola kuti Yehova akutsogolere panjira yako,+ Umudalire+ ndipo iye adzachitapo kanthu.+   Iye adzaonetsa poyera kulungama kwako kuti kuunike ngati kuwala,+ Adzaonetsa poyera chilungamo chako kuti chiwale ngati usana.+ ד [Da′leth]   Khala chete pamaso pa Yehova,+ Ndipo umuyembekezere ndi mtima wako wonse.+ Usapse mtima ndi aliyense amene zinthu zikumuyendera bwino,+ Munthu amene akukwaniritsa zolinga zake zoipa.+ ה [Heʼ]   Usapse mtima ndipo pewa kukwiya.+ Usapse mtima kuti ungachite choipa.+   Pakuti ochita zoipa adzaphedwa.+ Koma oyembekezera Yehova ndi amene  adzalandire dziko lapansi.+ ו [Waw] 10  Patsala kanthawi kochepa, woipa sadzakhalakonso.+ Udzayang’ana pamene anali kukhala, ndipo sadzapezekapo.+ 11  Koma anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi,+ Ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.+ ז [Za′yin] 12  Woipa akukonzera chiwembu munthu wolungama,+ Ndipo akumukukutira mano.+ 13  Koma Yehova adzamuseka,+ Pakuti akuona kuti chimaliziro chake chifika.+ ח [Chehth] 14  Oipa asolola lupanga ndipo akunga uta wawo,+ Kuti agwetse osautsika ndi osauka,+ Kuti aphe anthu amene njira zawo ndi zowongoka.+ 15  Lupanga lawo lidzalowa mumtima mwawo,+ Ndipo mauta awo adzathyoka.+ ט [Tehth] 16  Zinthu zochepa za munthu wolungama ndi zabwino+ Kusiyana ndi zinthu zochuluka za anthu ambiri oipa.+ 17  Pakuti manja a anthu oipa adzathyoledwa,+ Koma Yehova adzathandiza anthu olungama.+ י [Yohdh] 18  Yehova amadziwa za moyo wa anthu osalakwa,+ Ndipo cholowa chawo chidzakhalapo mpaka kalekale.+ 19  Pa nthawi yatsoka sadzachita manyazi,+ Ndipo pa nthawi ya njala adzakhuta.+ כ [Kaph] 20  Pakuti anthu oipa adzatheratu onse,+ Ndipo adani a Yehova adzafanana ndi busa la msipu wobiriwira mochititsa kaso. Iwo adzatha.+ Adzazimiririka ndi kusanduka utsi.+ ל [La′medh] 21  Munthu woipa amakongola zinthu za ena koma osabweza,+ Koma wolungama amakomera mtima ena ndipo amapereka mphatso.+ 22  Anthu amene Mulungu akuwadalitsa adzalandira dziko lapansi,+ Koma amene wawatemberera adzaphedwa.+ מ [Mem] 23  Yehova walimbitsa mapazi a munthu wamphamvu zake,+ Ndipo Mulungu amakondwera ndi njira zake.+ 24  Ngakhale atapunthwa, sadzagweratu,+ Pakuti Yehova wamugwira dzanja.+ נ [Nun] 25  Ndinali mwana, ndipo tsopano ndakula,+ Koma sindinaonepo munthu aliyense wolungama atasiyidwa,+ Kapena ana ake akupemphapempha chakudya.+ 26  Tsiku lililonse amakomera mtima ena ndi kuwakongoza zinthu,+ Ndipo ana ake adzalandira madalitso.+ ס [Sa′mekh] 27  Patuka pa choipa ndipo uchite chabwino,+ Ukatero udzakhala padziko lapansi mpaka kalekale.+ 28  Pakuti Yehova amakonda chilungamo,+ Ndipo sadzasiya anthu ake okhulupirika.+ ע [ʽA′yin]Adzawateteza mpaka kalekale.+ Koma ana a anthu oipa adzaphedwa.+ 29  Olungama adzalandira dziko lapansi,+ Ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.+ פ [Peʼ] 30  Pakamwa pa munthu wolungama pamalankhula zinthu zanzeru,+ Ndipo lilime lake limalankhula zinthu zachilungamo.+ 31  Chilamulo cha Mulungu wake chili mumtima mwake.+ Poyenda mapazi ake sadzaterereka.+ צ [Tsa·dheh′] 32  Woipa amalondalonda munthu wolungama,+ Ndipo amafuna kuti amuphe.+ 33  Koma Yehova sadzasiya wolungama m’manja mwa woipayo,+ Ndipo pamene wolungamayo akuweruzidwa, Mulungu sadzamuona monga wolakwa.+ ק [Qohph] 34  Yembekezera Yehova, ndi kusunga njira zake,+ Ndipo adzakukweza kuti ulandire dziko lapansi.+ Pamene oipa akuphedwa, iwe udzaona.+ ר [Rehsh] 35  Ine ndaona munthu woipa, wolamulira mwankhanza+ Zinthu zikumuyendera bwino ngati mtengo waukulu wa masamba obiriwira bwino panthaka yake.+ 36  Koma anafa ndipo sanapezekenso.+ Ndinamufunafuna ndipo sindinamupeze.+ ש [Shin] 37  Ona munthu wosalakwa ndipo yang’anitsitsa munthu wolungama,+ Pakuti tsogolo la munthu ameneyu ndi lamtendere.+ 38  Koma anthu onse ochimwa adzafafanizidwa.+ M’tsogolo, anthu oipa adzaphedwa.+ ת [Taw] 39  Chipulumutso cha anthu olungama chimachokera kwa Yehova.+ Iye ndi malo awo achitetezo champhamvu pa nthawi ya nsautso.+ 40  Yehova adzawathandiza ndi kuwapulumutsa.+ Adzawapulumutsa kwa anthu oipa ndi kuwalanditsa,+ Chifukwa athawira kwa iye.+

Mawu a M'munsi