Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 36:1-12

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide, mtumiki wa Yehova. 36  Uchimo ukulankhula mumtima mwa munthu woipa.+ Maso ake saona chifukwa choopera Mulungu.+   Pakuti amadzinyenga yekha,+ Ndipo sazindikira cholakwa chake ndi kudana nacho.+   Mawu a pakamwa pake ndi opweteka ndi achinyengo.+ Wasiya kugwiritsa ntchito nzeru zomuthandiza kuchita zinthu zabwino.+   Ali pabedi lake amakonza chiwembu kuti apweteke anzake.+ Amaima panjira yoipa.+ Sapewa kuchita zinthu zoipa.+   Inu Yehova, kukoma mtima kwanu kosatha kuli kumwamba.+ Kukhulupirika kwanu kwafika m’mitambo.+   Inu Mulungu, chilungamo chanu chili ngati mapiri anu.+ Chiweruzo chanu ndi chozama kwambiri ngati madzi akuya.+ Inu Yehova, mumapulumutsa munthu ndiponso nyama.+   Inu Mulungu, kukoma mtima kwanu kosatha ndi kwamtengo wapatali!+ Ndipo ana a anthu amabisala mu mthunzi wa mapiko anu.+   Amadya ndi kukhuta chakudya chonona m’nyumba mwanu.+ Ndipo mumawamwetsa mumtsinje wa zosangalatsa zanu zambiri.+   Pakuti inu ndinu kasupe wa moyo.+ Chifukwa cha kuwala kochokera kwa inu, tikuona kuwala.+ 10  Pitirizani kusonyeza kukoma mtima kwanu kosatha kwa anthu okudziwani,+ Ndiponso chilungamo  chanu kwa anthu owongoka mtima.+ 11  Musalole kuti phazi la anthu odzikweza lindipondereze.+ Ndipo musalole dzanja la anthu oipa kundipitikitsa kuti ndikhale wothawathawa.+ 12  Onani, ochita zinthu zopweteka anzawo agwa.+ Awakanikizira pansi ndipo sakuthanso kudzuka.+

Mawu a M'munsi