Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 35:1-28

Salimo la Davide. 35  Weruzani mlandu wanga inu Yehova, motsutsana ndi adani anga.+ Menyani nkhondo ndi kugonjetsa amene akumenyana ndi ine.+   Tengani chishango chaching’ono ndi chishango chachikulu,+ Ndipo bwerani kuti mundithandize.+   Tengani mkondo ndi nkhwangwa ya pankhondo kuti mukumane ndi anthu amene akundilondalonda.+ Uzani moyo wanga kuti: “Ine ndine chipulumutso chako.”+   Amene akufunafuna moyo wanga achite manyazi ndi kunyozeka.+ Amene akundikonzera chiwembu muwabweze ndipo athedwe nzeru.+   Akhale ngati mankhusu ouluzika ndi mphepo,+ Mngelo wa Yehova awapitikitse.+   Njira yawo ikhale ya mdima ndi yoterera,+ Ndipo mngelo wa Yehova aziwathamangitsa.   Iwo andikumbira mbuna popanda chifukwa ndi kuikapo ukonde,+ Akumba mbunazo kuti ndigweremo ngakhale kuti sindinalakwe.+   Awonongeke pamene iwo sakuyembekezera,+ Akodwe mu ukonde umene atchera okha.+ Agweremo ndi kuwonongeka.+   Koma moyo wanga ukondwere mwa Yehova.+ Usangalale chifukwa cha chipulumutso chake.+ 10  Ndinene ndi mtima wanga wonse kuti:+ “Inu Yehova, ndani angafanane ndi inu,+ Amene mumalanditsa wosautsika m’manja mwa munthu wamphamvu kuposa iyeyo,+ Amene mumalanditsa wozunzika ndi wosauka m’manja mwa munthu amene akumulanda zinthu zake?”+ 11  Mboni zachiwawa zimaimirira.+ Zimandifunsa zinthu zimene sindikudziwa.+ 12  Adani anga amandibwezera zoipa m’malo mwa zabwino,+ Ndipo ndimakhala wachisoni ngati wofedwa.+ 13  Iwo akadwala ndinali kuvala chiguduli,+ Ndinali kusautsa moyo wanga mwa kusala kudya.+ Ndipo mapemphero anga anali kubwerera kwa ine osayankhidwa.+ 14  Chifukwa cha mnzanga ndiponso m’bale wanga,+ Ndinamva chisoni kwambiri ngati munthu wolira maliro a mayi ake.+ Ndinawerama chifukwa cha chisoni. 15  Atandiona ndikuyenda motsimphina anasangalala ndipo anasonkhana pamodzi.+ Anasonkhana pamodzi kuti alimbane nane.+ Anandimenya pamene sindinali kuyembekezera.+ Anandikhadzulakhadzula ndipo sanakhale chete.+ 16  Anthu ampatuko amene anali kunditonza kuti apeze kachakudya,+ Anandikukutira mano.+ 17  Inu Yehova, kodi mudzayang’anira zimenezi kufikira liti?+ Ndipulumutseni kwa anthu ofuna kundiwononga,+ Pulumutsani moyo wanga+ ku mikango yamphamvu. 18  Ndidzakutamandani mu mpingo waukulu.+ Ndidzakutamandani pakati pa anthu ambiri.+ 19  Musalole kuti anthu amene amadana ndi ine popanda chifukwa akondwere ndi kusautsika kwanga.+ Ndipo musalole kuti anthu amene amandida popanda chifukwa anditsinzinire diso.+ 20  Iwo salankhula mawu amtendere,+ Koma amakonzera chiwembu anthu ofatsa a padziko lapansi, Kuti awachitire zachinyengo.+ 21  Amatsegula kwambiri pakamwa pawo kuti atsutsane nane.+ Iwo amati: “Eya! Eya! Tadzionera tokha.”+ 22  Inu Yehova, mwaona zimenezi+ ndipo musakhale chete.+ Musakhale patali ndi ine, inu Yehova.+ 23  Nyamukani ndi kukhala maso kuti mundichitire chilungamo,+ Chitani zimenezi inu Mulungu wanga Yehova, kuti muweruze mlandu wanga.+ 24  Inu Yehova Mulungu wanga, mundiweruze mogwirizana ndi chilungamo chanu,+ Musalole kuti adani anga akondwere ndi kusautsika kwanga.+ 25  Musalole kuti mumtima mwawo anene kuti: “Eya! Izi ndi zimene timafuna.”+ Ndipo asanene kuti: “Tamumeza.”+ 26  Onse amene akukondwera ndi tsoka langa,+ Achite manyazi ndi kuthedwa nzeru.+ Onse odzikweza pamaso panga achite manyazi+ ndi kutsitsidwa.+ 27  Onse amene amakonda chilungamo changa afuule mosangalala ndi kukondwera.+ Nthawi zonse azinena kuti:+ “Alemekezeke Yehova, amene amasangalala mtumiki wake akakhala pa mtendere.”+ 28  Lilime langa linene chapansipansi za chilungamo chanu,+ Ndipo likutamandeni tsiku lonse.+

Mawu a M'munsi