Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 34:1-22

Salimo la Davide, pa nthawi imene anachita zinthu ngati wamisala+ pamaso pa Abimeleki* moti anam’pitikitsa ndipo Davideyo anathawa. א [ʼAʹleph] 34  Ndidzatamanda Yehova nthawi zonse.+ Ndidzamutamanda ndi pakamwa panga mosalekeza.+ ב [Behth]   Ndidzadzitamandira mwa Yehova.+ Ofatsa adzamva ndi kukondwera.+ ג [Giʹmel]   Lemekezani Yehova pamodzi ndi ine+ anthu inu, Tiyeni tonse tikweze dzina lake.+ ד [Daʹleth]   Ndinafunsa kwa Yehova ndipo iye anandiyankha,+ Pakuthawathawa kwanga konse iye anandilanditsa.+ ה [Heʼ]   Amene anamukhulupirira anasangalala,+ Ndipo nkhope zawo sizinachite manyazi.+ ז [Zaʹyin]   Wosautsikayu anaitana ndipo Yehova anamva.+ Anamupulumutsa m’masautso ake onse.+ ח [Chehth]   Mngelo wa Yehova amamanga msasa mozungulira onse oopa Mulungu,+ Ndipo amawapulumutsa.+ ט [Tehth]   Anthu inu, talawani ndipo muona kuti Yehova ndi wabwino.+ Wodala ndi munthu wamphamvu amene amathawira kwa iye.+ י [Yohdh]   Opani Yehova, inu oyera ake,+ Pakuti onse omuopa sasowa kanthu.+ כ [Kaph] 10  Mikango yamphamvu ingakhale ndi chakudya chochepa ndipo ingamve njala.+ Koma ofunafuna Yehova sadzasowa chilichonse chabwino.+ ל [Laʹmedh] 11  Bwerani kuno ana anga, ndimvetsereni.+ Ndikuphunzitsani kuopa Yehova.+ מ [Mem] 12  Kodi munthu wokonda moyo ndani,+ Amene akufuna kukhala ndi moyo wabwino kwa masiku ambiri?+ נ [Nun] 13  Tetezani lilime lanu ku zinthu zoipa,+ Ndi milomo yanu kuti isalankhule chinyengo.+ ס [Saʹmekh] 14  Patukani pa zinthu zoipa ndipo chitani zabwino.+ Funafunani mtendere ndi kuusunga.+ ע [ʽAʹyin] 15  Maso a Yehova ali pa olungama,+ Ndipo makutu ake amamva kufuula kwawo kopempha thandizo.+ פ [Peʼ] 16  Nkhope ya Yehova imakwiyira anthu ochita zoipa,+ Kuti dzina lawo lisatchulidwenso padziko lapansi.+ צ [Tsa·dhehʹ] 17  Olungama anafuula, ndipo Yehova anamva,+ Iye anawapulumutsa m’masautso awo onse.+ ק [Qohph] 18  Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka.+ Ndipo odzimvera chisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.+ ר [Rehsh] 19  Masoka a munthu wolungama ndi ochuluka,+ Koma Yehova amamupulumutsa ku masoka onsewo.+ ש [Shin] 20  Amateteza mafupa onse a wolungamayo. Ndipo palibe fupa ngakhale limodzi limene lathyoledwa.+ ת [Taw] 21  Masoka adzapha munthu woipa.+ Ndipo wodana ndi munthu wolungama adzapezeka wolakwa.+ 22  Yehova amawombola moyo wa atumiki ake.+ Ndipo palibe aliyense wothawira kwa iye amene adzapezeka wolakwa.+

Mawu a M'munsi

Zikuoneka kuti ili ndi dzina laudindo la Mfumu Akisi. Yerekezerani ndi mawu a m’munsi pa Ge 20:2.