Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 33:1-22

33  Fuulani mosangalala chifukwa cha Yehova, inu nonse olungama.+ M’poyenera kuti owongoka mtima atamande Mulungu.+   Yamikani Yehova poimba zeze.+ Muimbireni nyimbo zomutamanda ndi choimbira cha zingwe 10.+   Muimbireni nyimbo yatsopano.+ Muimbireni choimbira cha zingwe ndi mtima wonse ndi kufuula mosangalala.+   Pakuti mawu a Yehova ndi owongoka,+ Ndipo ntchito zake zonse ndi zodalirika.+   Iye amakonda chilungamo ndi chiweruzo chosakondera.+ Dziko lapansi ladzaza ndi kukoma mtima kosatha kwa Yehova.+   Kumwamba kunalengedwa ndi mawu a Yehova,+ Ndipo makamu ake onse analengedwa ndi mpweya wa m’kamwa mwake.+   Anasonkhanitsa madzi a m’nyanja ngati wachita kuwatchinga ndi khoma,+ Anaika madzi amphamvu m’nyumba zosungiramo zinthu.   Onse okhala padziko lapansi aope Yehova.+ Anthu onse okhala panthaka ya dziko lapansi achite naye mantha.+   Pakuti iye ananena, ndipo zinachitika.+ Iye analamula, ndipo zinakhalapo.+ 10  Yehova wasokoneza zolinga za anthu a mitundu ina.+ Walepheretsa maganizo a mitundu ya anthu.+ 11  Zolinga za Yehova zidzakhalapo mpaka kalekale.+ Maganizo a mumtima mwake adzakhalapo ku mibadwomibadwo.+ 12  Wodala ndi mtundu umene Mulungu wawo ndi Yehova,+ Anthu amene iye wawasankha kukhala cholowa chake.+ 13  Kuchokera kumwamba, Yehova wayang’ana,+ Waona ana onse a anthu.+ 14  Kuchokera kumalo achikhalire kumene iye amakhala,+ Wayang’anitsitsa onse okhala padziko lapansi. 15  Iye akuumba mtima wa aliyense wa iwo.+ Akulingalira ntchito zawo zonse.+ 16  Palibe mfumu imene inapulumuka chifukwa cha kukula kwa gulu lake lankhondo.+ Munthu wamphamvu sapulumuka chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu zake.+ 17  Hatchi siingabweretse chipulumutso,+ Siingapulumutse munthu chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu zake.+ 18  Taonani! Diso la Yehova lili pa anthu amene amamuopa,+ Amene amayembekezera kukoma mtima kwake kosatha,+ 19  Kuti apulumutse moyo wawo ku imfa,+ Ndi kuwasunga ndi moyo pa nthawi ya njala.+ 20  Moyo wathu wakhala ukuyembekeza Yehova.+ Iye ndi mthandizi wathu ndi chishango chathu.+ 21  Mitima yathu imakondwera mwa iye.+ Pakuti timadalira dzina lake loyera.+ 22  Inu Yehova, kukoma mtima kwanu kosatha kukhale pa ife,+ Pakuti takhala tikuyembekezera inu.+

Mawu a M'munsi