Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 32:1-11

Salimo la Davide. Masikili.* 32  Wodala ndi munthu amene wakhululukidwa zolakwa zake, amene machimo ake aphimbidwa.+   Wodala ndi munthu amene Yehova sanamusungire cholakwa chake,+ Amene alibe mtima wachinyengo.+   Pamene ndinakhala chete osaulula machimo anga, mafupa anga anafooka, chifukwa tsiku lonse ndinali kuvutika mumtima mwanga.+   Pakuti dzanja lanu linali kundilemera usana ndi usiku.+ Mphamvu zanga zinauma ngati madzi m’nyengo yotentha ya chilimwe.+ [Seʹlah.]   Pamapeto pake ndinaulula tchimo langa kwa inu, ndipo sindinabise cholakwa changa.+ Ndinati: “Ndidzaulula kwa Yehova machimo anga.”+ Ndipo inu munandikhululukira zolakwa zanga ndi machimo anga.+ [Seʹlah.]   Pa chifukwa chimenechi, aliyense wokhulupirika adzapemphera kwa inu,+ Pa nthawi imene inu mungapezeke.+ Ndipo madzi ambiri osefukira sadzamukhudza ngakhale pang’ono.+   Ndinu malo anga obisalamo, mudzanditeteza ku masautso.+ Mudzachititsa kuti chisangalalo chindizungulire pamene mukundipulumutsa.+ [Seʹlah.]   Inu munati: “Ndidzakupatsa nzeru ndi kukulangiza njira yoti uyendemo.+ Ndidzakupatsa malangizo ndi kukuyang’anira.+   Anthu inu, musakhale ngati hatchi kapena nyulu* yosazindikira,+ Imene munthu amachita kuimanga chingwe chapakamwa ndi chapamutu kuti athetse kupulupudza kwake,+ Ndi kuti aiyandikire.”+ 10  Zopweteka za woipa ndi zambiri. Koma wokhulupirira Yehova+ amazunguliridwa ndi kukoma mtima kosatha.+ 11  Inu olungama, kondwerani chifukwa cha zimene Yehova wachita ndipo sangalalani.+ Fuulani ndi chisangalalo inu nonse owongoka mtima.+

Mawu a M'munsi

“Masikili” ndi mawu achiheberi amene tanthauzo lake silikudziwika. N’kutheka kuti amatanthauza “ndakatulo imene munthu amanena posinkhasinkha.”
Onani mawu a m’munsi pa 2Sa 13:29.