Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 31:1-24

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide. 31  Ndathawira kwa inu Yehova.+ Musalole kuti ndichite manyazi.+ Ndipulumutseni chifukwa cha chilungamo chanu.+   Tcherani khutu lanu kwa ine.+ Ndilanditseni mofulumira.+ Mukhale thanthwe lolimba kwa ine,+ Mukhale nyumba ya mpanda wolimba kuti mundipulumutse.+   Pakuti inu ndinu thanthwe langa ndi malo anga achitetezo.+ Chifukwa cha dzina lanu+ mudzanditsogolera ndi kundilozera njira.+   Mudzandiwonjola mu ukonde umene anditchera,+ Pakuti inu ndinu malo anga achitetezo.+   Ndikuikiza mzimu* wanga m’manja mwanu.+ Mwandiwombola,+ inu Yehova, Mulungu wachoonadi.+   Ndimadana ndi olambira mafano opanda pake ndi achabechabe.+ Koma ine ndimadalira Yehova.+   Ndidzakondwera ndi kusangalala chifukwa cha kukoma mtima kwanu kosatha,+ Pakuti mwaona kusautsika kwanga.+ Mwadziwa zowawa zimene zandigwera,+   Simunandipereke m’manja mwa adani.+ Mwapondetsa phazi langa pamalo otakasuka.+   Ndikomereni mtima inu Yehova, pakuti ndasautsika kwambiri.+ Diso langa lafooka chifukwa cha chisoni,+ chimodzimodzinso moyo wanga ndi m’mimba mwanga.+ 10  Chifukwa cha chisoni, moyo wanga watha,+ Ndipo chifukwa cha kuusa moyo kwanga, zaka zanga zafika kumapeto.+ Chifukwa cha zolakwa zanga, mphamvu zanga zafooka,+ Ndipo mafupa anga afooka.+ 11  Ndakhala chitonzo+ pamaso pa onse odana nane,+ Ndipo kwa anthu oyandikana nawo ndakhala chitonzo chachikulu,+ Kwa anthu ondidziwa ndakhala woopsa.+ Akandiona ndili panja amandithawa.+ 12  Ndaiwalidwa ngati munthu wakufa amene anthu sakumukumbukiranso.+ Ndakhala ngati chiwiya chosweka.+ 13  Ndamva zinthu zoipa zimene anthu ambiri akunena,+ Ndamva zochititsa mantha kuchokera kumbali zonse.+ Akasonkhana pamodzi kundichitira upo,+ Amakonza chiwembu kuti achotse moyo wanga.+ 14  Koma ine chikhulupiriro changa chili mwa inu Yehova.+ Ndipo ndikunena kuti: “Inu ndinu Mulungu wanga.”+ 15  Moyo wanga uli m’manja mwanu.+ Ndilanditseni m’manja mwa adani anga ndi kwa anthu ondisakasaka.+ 16  Ndikomereni mtima ine mtumiki wanu.+ Ndipulumutseni mwa kukoma mtima kwanu kosatha.+ 17  Inu Yehova, musalole kuti ndichite manyazi, pakuti ndaitana pa dzina lanu.+ Anthu oipa achite manyazi.+ Akhale chete m’Manda.+ 18  Milomo yachinyengo isowe chonena,+ Milomo imene ikulankhula motsutsana ndi wolungama,+ yosadziletsa pa kudzikweza ndi kunyoza ena.+ 19  Ubwino wanu,+ umene mwasungira anthu okuopani ndi wochuluka kwambiri!+ Ubwino umenewu mwapereka kwa anthu othawira kwa inu. Mwaupereka kwa iwo, ana a anthu akuona.+ 20  Mudzawabisa m’malo otetezeka pafupi ndi inu,+ Kuwachotsa pamaso pa anthu amene asonkhana pamodzi kuti awachitire chiwembu.+ Mudzawabisa mumsasa wanu kwa anthu ofuna kukangana nawo.+ 21  Yehova adalitsike,+ Pakuti wandisonyeza modabwitsa kukoma mtima kosatha+ mumzinda wozingidwa ndi adani.+ 22  Koma ine nditapanikizika ndinati:+ “Ndidzafafanizidwa kuchoka pamaso panu.”+ Ndithudi mwamva kuchonderera kwanga pamene ndinali kufuulira kwa inu kupempha thandizo.+ 23  Kondani Yehova, inu nonse okhulupirika ake.+ Yehova amateteza okhulupirika,+ Koma aliyense wodzikuza adzamulanga mowirikiza.+ 24  Limbani mtima ndipo muchite zinthu mwamphamvu,+ Inu nonse amene mukuyembekezera Yehova.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 4.