Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Masalimo 30:1-12

Nyimbo ndi Salimo la Davide lotsegulira nyumba.+ 30  Ndidzakutamandani inu Yehova, pakuti mwandipulumutsa,+ Ndipo simunalole kuti adani anga akondwere ndi kusautsika kwanga.+   Inu Yehova Mulungu wanga, ndinafuulira kwa inu kuti mundithandize ndipo munandichiritsa.+   Inu Yehova, mwanditulutsa m’Manda,+ Mwandisunga ndi moyo, kuti ndisatsikire m’dzenje.+   Imbani nyimbo zotamanda Yehova, inu okhulupirika ake,+ Yamikani dzina lake loyera.*+   Chifukwa mkwiyo wa Mulungu sukhalitsa pa munthu,+ Koma kukoma mtima kwake ndi kwa moyo wonse.+ Usiku kumakhala kulira,+ koma m’mawa kumakhala kufuula ndi chisangalalo.+   Mtima wanga utakhazikika ndinati:+ “Sindidzagwedezeka.”+   Inu Yehova, chifukwa chakuti munandikomera mtima munakhazikitsa mwamphamvu phiri langa.+ Pamene munabisa nkhope yanu, ndinasokonezeka.+   Ndinaitana inu Yehova,+ Ndipo ndinachonderera Yehova kuti andikomere mtima.+   Kodi magazi anga angakhale ndi phindu lanji ngati nditatsikira kudzenje la manda?+ Kodi fumbi lidzakutamandani?+ Kodi lidzalengeza kuti inu ndinu woona?+ 10  Imvani inu Yehova, ndi kundikomera mtima.+ Inu Yehova, khalani mthandizi wanga.+ 11  Mwasintha kulira kwanga kuti kukhale kuvina.+ Mwandivula chiguduli* changa ndipo mwandiveka chisangalalo,+ 12  Kuti mtima wanga uimbe nyimbo zokutamandani ndipo usakhale chete.+ Inu Yehova Mulungu wanga, ndidzakutamandani mpaka kalekale.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “chikumbutso chake choyera.”
Ena amati “saka.”