Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 3:1-8

Nyimbo ya Davide pamene anali kuthawa mwana wake Abisalomu.+ 3  Inu Yehova, n’chifukwa chiyani adani anga achuluka chotere?+ N’chifukwa chiyani anthu ondiukira achuluka?+   Ponena za moyo wanga, ambiri akuti: “Mulungu sam’pulumutsa ameneyu.”+ [Seʹlah.*]   Koma inu Yehova ndinu chishango changa,+ Ulemerero wanga+ ndiponso Wonditukula mutu.+   Ndidzafuulira Yehova mokweza, Ndipo iye adzandiyankha m’phiri lake loyera.+ [Seʹlah.]   Koma ine ndidzagona pansi ndi kupeza tulo. Ndidzadzuka ndithu, pakuti Yehova amandithandiza.+   Sindidzaopa anthu masauzande makumimakumi Amene andiukira ndi kundizungulira.+   Nyamukani,+ inu Yehova! Ndipulumutseni+ inu Mulungu wanga!+ Pakuti mudzakantha adani anga onse pachibwano.+ Mano a anthu oipa mudzawaphwanyaphwanya.+   Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.+ Madalitso anu ali pa anthu anu.+ [Seʹlah.]

Mawu a M'munsi

“Seʹlah” ndi mawu achiheberi amene anali kuwagwiritsa ntchito polemba nyimbo kapena ndakatulo. Tanthauzo lake lenileni silikudziwika.