Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 29:1-11

Salimo la Davide. 29  M’patseni Yehova, inu amphamvu,* M’patseni Yehova ulemerero ndipo vomerezani kuti iye ndi wamphamvu.+   M’patseni Yehova ulemerero woyenera dzina lake.+ Weramirani Yehova mutavala zovala zopatulika zokongola.+   Liwu la Yehova lili pamwamba pa madzi,*+ Liwu la Mulungu waulemerero+ lagunda ngati bingu.+ Yehova ali pamwamba pa madzi ambiri.+   Liwu la Yehova ndi lamphamvu,+ Liwu la Yehova ndi lokwezeka.+   Liwu la Yehova likuthyola mitengo ya mkungudza, Yehova akuthyolathyola mitengo ya mkungudza ya ku Lebanoni.+   Iye akuichititsa kudumphadumpha ngati mwana wa ng’ombe,+ Lebanoni ndi Sirioni+ akudumphadumpha ngati ana a ng’ombe zakutchire.   Liwu la Yehova likutulutsa malawi a moto.+   Liwu la Yehova likuchititsa chipululu kuphiriphitha,+ Yehova akuchititsa chipululu cha Kadesi+ kuphiriphitha.   Liwu la Yehova likuchititsa mbawala zazikazi kuphiriphitha ndi ululu wa pobereka,+ Ndipo likufafaniza nkhalango.+ M’kachisi wake aliyense akunena kuti: “Ulemerero ndi wa Mulungu!”+ 10  Yehova wakhala pampando wake wachifumu pamwamba pa chigumula,*+ Ndipo Yehova ndi mfumu mpaka kalekale.+ 11  Yehova adzapatsa anthu ake mphamvu.+ Yehova adzadalitsa anthu ake ndi mtendere.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “ana a amphamvu.”
“Madzi” amenewa akutanthauza “mvula yamkuntho.”
Kapena kuti “pamwamba pa nyanja yaikulu ya kumwamba.”