Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 28:1-9

Salimo la Davide. 28  Ndikuitana inu Yehova.+ Inu Thanthwe langa, musatseke makutu anu pamene ine ndikuitana,+ Kuti musakhale chete pamaso panga,+ Kutinso ine ndisafanane ndi amene akutsikira kudzenje la manda.+   Imvani mawu anga ochonderera pamene ndikufuulira inu kuti mundithandize, Pamene ndikukweza manja anga,+ nditayang’ana kumene kuli chipinda chamkati cha m’malo anu opatulika.+   Musandikokolole pamodzi ndi anthu oipa komanso anthu amene amachita zopweteka anzawo,+ Anthu amene amalankhula mawu amtendere ndi anzawo+ koma m’mitima yawo muli zinthu zoipa.+   Muwabwezere mogwirizana ndi zochita zawo,+ Mogwirizana ndi kuipa kwa zochita zawo.+ Abwezereni mogwirizana ndi ntchito za manja awo.+ Abwezereni zochita zawo.+   Pakuti iwo salabadira zochita za Yehova,+ Kapena ntchito za manja ake.+ Mulungu sadzawamanga koma adzawapasula.   Adalitsike Yehova, chifukwa wamva kuchonderera kwanga.+   Yehova ndiye mphamvu yanga+ ndi chishango changa.+ Mtima wanga umam’khulupirira.+ Iye wandithandiza, moti mtima wanga ukukondwera.+ Ndidzamutamanda mwa kumuimbira nyimbo yanga.+   Yehova ndiye mphamvu kwa anthu ake,+ Iye ndi malo achitetezo odzetsa chipulumutso chachikulu kwa wodzozedwa wake.+   Pulumutsani anthu anu, ndipo dalitsani cholowa chanu.+ Mukhale m’busa wawo ndipo muwanyamule mpaka kalekale.+

Mawu a M'munsi