Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 27:1-14

Salimo la Davide. 27  Yehova ndiye kuwala+ kwanga ndi chipulumutso changa.Ndingaopenso ndani?+Yehova ndiye malo a chitetezo cha moyo wanga.+Ndingachitenso mantha ndi ndani?+   Anthu ochita zoipa atandiyandikira kuti adye mnofu wanga,+Popeza kuti iwo ndi ondiukira komanso adani anga,+Anapunthwa ndi kugwa.+   Ngakhale gulu lankhondo litamanga msasa kuti lindiukire,+Mtima wanga sudzachita mantha.Ngakhale nkhondo yolimbana ndi ine itayambika,Pameneponso ndidzadalira Mulungu.+   Chinthu chimodzi chimene ndapempha kwa Yehova,+Chimenecho ndi chimene ndimachikhumba,+N’chakuti, ndikhale m’nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga,+Kuti ndione ubwino wa Yehova,+Komanso kuti ndiyang’ane kachisi wake moyamikira.   Pakuti pa tsiku la tsoka, iye adzandibisa m’malo ake otetezeka.+Adzandibisa m’malo obisika m’hema wake.+Adzandiika pamwamba, pathanthwe.+   Pamenepo mutu wanga udzakwezeka pamwamba pa adani onse ondizungulira.Ndipo ndidzapereka nsembe za kufuula mokondwera pahema wake.+Ndidzamuimbira nyimbo, ndithu ndidzaimba nyimbo zotamanda Yehova.+   Inu Yehova, imvani mawu anga pamene ndikuitana.+Ndikomereni mtima ndi kundiyankha.+   Mtima wanga wanena lamulo lanu lakuti: “Ndifunefuneni anthu inu.”+Ndidzakufunafunani, inu Yehova.+   Musandibisire nkhope yanu.+Musabweze mtumiki wanu mutakwiya.+Inu mukhale mthandizi wanga.Musanditaye ndi kundisiya, inu Mulungu wa chipulumutso changa.+ 10  Ngakhale bambo anga ndi mayi anga atandisiya,+Yehova adzanditenga.+ 11  Ndilangizeni, inu Yehova, kuti ndiyende m’njira yanu.Nditsogolereni m’njira yowongoka kuti nditetezeke kwa adani anga. 12  Musandipereke kwa adani anga.+Pakuti mboni zonama zandiukira,+Chimodzimodzinso munthu wachiwawa.+ 13  Ngati ndikanakhala wopanda chikhulupiriro poona ubwino wa Yehova m’dziko la anthu amoyo, ndikanataya chiyembekezo.+ 14  Yembekezera Yehova.+ Limba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu.+Yembekezera Yehova.+

Mawu a M'munsi