Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 26:1-12

Salimo la Davide. 26  Ndiweruzeni,+ inu Yehova, pakuti ine ndayenda mogwirizana ndi mtima wanga wosagawanika,+ Ndipo ndikudalira Yehova kuti ndisagwedezeke.+   Ndisanthuleni, inu Yehova, ndi kundiyesa.+ Yengani impso zanga ndi mtima wanga.+   Pakuti kukoma mtima kwanu kosatha kuli pamaso panga. Ine ndayenda m’choonadi chanu.+   Sindinakhale pansi pamodzi ndi anthu achinyengo.+ Ndipo sindinayanjane ndi anthu obisa umunthu wawo.+   Ndimadana ndi mpingo wa anthu ochita zoipa,+ Ndipo sindikhala pansi ndi anthu oipa.+   Ndidzasamba m’manja mwanga kusonyeza kuti ndine wopanda cholakwa,+ Ndipo ndidzayenda mozungulira guwa lanu lansembe, inu Yehova,+   Kuti mawu anga oyamikira amveke kwambiri,+ Ndi kulengeza ntchito zanu zonse zodabwitsa.+   Yehova, ine ndimakonda nyumba imene inu mumakhala+ Ndi malo amene kumakhala ulemerero wanu.+   Musachotse moyo wanga pamodzi ndi anthu ochimwa,+ Kapena pamodzi ndi anthu a mlandu wamagazi.+ 10  M’manja mwa anthu amenewa muli khalidwe lotayirira,+ Ndipo m’dzanja lawo lamanja mwadzaza ziphuphu.+ 11  Koma ine ndidzayenda mogwirizana ndi mtima wanga wosagawanika.+ Ndiwomboleni+ ndi kundikomera mtima.+ 12  Phazi langa lidzaimadi pamalo athyathyathya.+ Pamsonkhano, ndidzatamanda Yehova.+

Mawu a M'munsi