Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Masalimo 25:1-22

Salimo la Davide. א [ʼA′leph] 25  Ndapereka moyo wanga kwa inu Yehova.+ ב [Behth]   Inu Mulungu wanga, chikhulupiriro changa chili mwa inu.+ Musalole kuti ndichite manyazi. Adani anga asakondwere chifukwa cha masautso anga.+ ג [Gi′mel]   Ndithudi, palibe aliyense amene adzachita manyazi mwa anthu amene chiyembekezo chawo chili mwa inu.+ Amene adzachite manyazi ndi amene akuchita zinthu mwachinyengo koma osaphula kanthu.+ ד [Da′leth]   Ndidziwitseni njira zanu, inu Yehova.+ Ndiphunzitseni kuyenda m’njira zanu.+ ה [Heʼ]   Ndiyendetseni m’choonadi chanu ndi kundiphunzitsa,+ Pakuti inu ndinu Mulungu wa chipulumutso changa.+ ו [Waw]Chiyembekezo changa chili mwa inu tsiku lonse.+ ז [Za′yin]   Kumbukirani chifundo chanu,+ inu Yehova, ndi zochita zanu zosonyeza kukoma mtima kosatha.+ Pakuti munayamba kuchita zimenezo kale kwambiri.+ ח [Chehth]   Musakumbukire machimo a pa unyamata wanga ndi zolakwa zanga.+ Ndikumbukireni malinga ndi kukoma mtima kwanu kosatha,+ Ndiponso chifukwa cha ubwino wanu, inu Yehova.+ ט [Tehth]   Yehova ndi wabwino ndi wolungama.+ N’chifukwa chake amalangiza ochimwa kuti ayende m’njira yoyenera.+ י [Yohdh]   Adzachititsa ofatsa kutsatira zigamulo zake,+ Ndipo adzaphunzitsa ofatsa kuyenda m’njira yake.+ כ [Kaph] 10  M’njira zonse za Yehova muli kukoma mtima kosatha ndi choonadi Kwa anthu osunga pangano+ lake ndi zikumbutso zake.+ ל [La′medh] 11  Chifukwa cha dzina lanu, inu Yehova,+ Mundikhululukire cholakwa changa ngakhale kuti n’chachikulu.+ מ [Mem] 12  Tsopano munthu woopa Yehova ndani?+ Adzamulangiza kuyenda m’njira imene adzasankha.+ נ [Nun] 13  Moyo wake udzasangalala ndi ubwino wa Mulungu,+ Mbadwa zake zidzatenga dziko lapansi kukhala lawo.+ ס [Sa′mekh] 14  Ubwenzi wolimba ndi Yehova ndi wa anthu amene amamuopa,+ Pangano lakenso ndi la anthu oterowo, ndipo iye amawadziwitsa panganolo.+ ע [ʽA′yin] 15  Maso anga amayang’ana kwa Yehova nthawi zonse,+ Chifukwa iye ndi amene amawonjola phazi langa mu ukonde.+ פ [Peʼ] 16  Ndicheukireni ndi kundikomera mtima.+ Pakuti ndasungulumwa ndipo ndasautsika.+ צ [Tsa·dheh] 17  Masautso a mtima wanga awonjezeka.+ Ndilanditseni ku nkhawa zimene zili pa ine.+ ר [Rehsh] 18  Onani masautso anga ndi mavuto anga,+ Ndipo mundichotsere machimo anga onse.+ 19  Onani mmene adani anga achulukira,+ Ndipo chifukwa cha chidani chawo chachikulu, amafuna kundichitira chiwawa.+ ש [Shin] 20  Tetezani moyo wanga ndi kundilanditsa.+ Musalole kuti ndichite manyazi, pakuti ndathawira kwa inu.+ ת [Taw] 21  Mtima wanga wosagawanika ndiponso wowongoka unditeteze,+ Pakuti chiyembekezo changa chili mwa inu.+ 22  Inu Mulungu, wombolani Isiraeli m’masautso ake onse.+

Mawu a M'munsi