Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 24:1-10

Salimo la Davide. 24  Dziko lapansi ndi zonse zili mmenemo ndi za Yehova,+ Nthaka ndi yake pamodzi ndi onse okhala panthakapo.+   Iye anakhazika dziko lapansi molimba panyanja,+ Ndipo analikhazikitsa mwamphamvu pamitsinje.+   Ndani angakwere m’phiri la Yehova?+ Ndipo ndani anganyamuke kukalowa m’malo ake opatulika?+   Aliyense wopanda mlandu m’manja mwake ndi woyera mumtima mwake,+ Amene sanaone Moyo wanga ngati wopanda pake,+ Kapena kulumbira mwachinyengo.+   Ameneyo adzalandira madalitso kuchokera kwa Yehova,+ Adzalandira chilungamo kuchokera kwa Mulungu wa chipulumutso chake.+   Umenewo ndiwo m’badwo wa amene amafunafuna Mulungu, M’badwo wa anthu ofunafuna nkhope yanu, inu Mulungu wa Yakobo.+ [Seʹlah.]   “Tukulani mitu yanu, inu zipata,+ Ndipo dzitukuleni, inu makomo akale lomwe,+ Kuti Mfumu yaulemerero ilowe!”+   “Kodi Mfumu yaulemerero imeneyi ndani?”+ “Ndi Yehova, wanyonga ndi wamphamvu,+ Yehova wamphamvu mu nkhondo.”+   “Tukulani mitu yanu, inu zipata,+ Tukulani mitu, inu makomo akale lomwe, Kuti Mfumu yaulemerero ilowe!”+ 10  “Kodi Mfumu yaulemerero imeneyi ndani?” “Ndi Yehova wa makamu. Iye ndiye Mfumu yaulemerero.”+ [Seʹlah.]

Mawu a M'munsi