Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 23:1-6

Nyimbo ya Davide. 23  Yehova ndi M’busa wanga.+ Sindidzasowa kanthu.+   Amandigoneka m’mabusa a msipu wambiri.+ Amandiyendetsa m’malo opumira a madzi ambiri.+   Amatsitsimula moyo wanga.+ Amanditsogolera m’tinjira tachilungamo chifukwa cha dzina lake.+   Ngakhale ndikuyenda m’chigwa cha mdima wandiweyani,+ Sindikuopa kanthu,+ Pakuti inu muli ndi ine.+ Chibonga chanu ndi ndodo yanu ndi zimene zimandilimbikitsa.+   Mumandipatsa chakudya patebulo, pamaso pa anthu ondichitira zoipa.+ Mwadzoza mutu wanga ndi mafuta.+ Chikho changa ndi chodzaza bwino.+   Ndithudi, ubwino ndi kukoma mtima kosatha zidzanditsata masiku onse a moyo wanga.+ Ndipo ine ndidzakhala m’nyumba ya Yehova mpaka kalekale.+

Mawu a M'munsi