Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 22:1-31

Kwa wotsogolera nyimbo: Nyimboyi iimbidwe motsatira Mbawala Yaikazi ya M’bandakucha. Nyimbo ya Davide. 22  Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?+ N’chifukwa chiyani mukuchedwa kundipulumutsa?+ N’chifukwa chiyani simukumva mawu a kubuula kwanga?+   Inu Mulungu wanga, ine ndimaitana usana koma simundiyankha.+ Usiku ndimaitanabe, moti sindikukhala chete.+   Koma inu ndinu woyera.+ Mukukhala pakati pa zitamando za Isiraeli.+   Makolo athu anali kudalira inu.+ Iwo anali kudalira inu ndipo munali kuwapulumutsa.+   Iwo anali kufuulira inu,+ ndipo anali kupulumuka.+ Anali kudalira inu, ndipo simunawachititse manyazi.+   Koma ine ndine nyongolotsi+ osati munthu. Anthu amanditonza ndipo ndine wonyozeka kwa anthu.+   Anthu onse ondiona amandinyodola.+ Iwo amandinyogodola ndi pakamwa pawo, ndipo amapukusa mitu yawo mondinyoza.+ Iwo amati:   “Anadzipereka kwa Yehova.+ Amupulumutse Iyeyo!+ Ngati Mulungu amamukonda, amulanditse!”+   Pakuti ndinu amene munanditulutsa m’mimba,+ Amene munandichititsa kumva kuti ndine wotetezeka pamene ndinali kuyamwa mabere a mayi anga.+ 10  Ndinaponyedwa m’manja mwanu kuchokera m’mimba.+ Kuyambira ndili m’mimba mwa mayi anga, inu mwakhala Mulungu wanga.+ 11  Musakhale kutali ndi ine, chifukwa zondisautsa zili pafupi,+ Ndiponso chifukwa ndilibe mthandizi winanso.+ 12  Ng’ombe zazing’ono zamphongo zochuluka zandizungulira.+ Nkhunzi zamphamvu za ku Basana zandizinga.+ 13  Iwo anditsegulira pakamwa pawo mondiopseza,+ Ngati mkango wokhadzula nyama umenenso ukubangula.+ 14  Ndathiridwa pansi ngati madzi.+ Mafupa anga onse alekanalekana.+ Mtima wanga wakhala ngati phula,+ Wasungunuka mkati mwanga.+ 15  Mphamvu yanga yauma gwaa, ngati phale.+ Lilime langa lamamatira kunkhama zanga,+ Ndipo mwandikhazika m’fumbi la imfa.+ 16  Agalu andizungulira.+ Khamu la anthu ochita zoipa landizinga.+ Iwo akuluma manja ndi mapazi anga ngati mkango.+ 17  Ndingathe kuwerenga mafupa anga onse.+ Adaniwo akuona zimenezi, ndipo akundiyang’anitsitsa.+ 18  Iwo akugawana zovala zanga pakati pawo,+ Ndipo akuchita maere pazovala zanga.+ 19  Koma inu Yehova, musakhale kutali ndi ine,+ Inu mphamvu yanga,+ ndithandizeni mofulumira.+ 20  Landitsani moyo wanga ku lupanga,+ Moyo wanga wokhawu umene ndili nawo muulanditse m’kamwa mwa galu.+ 21  Ndipulumutseni m’kamwa mwa mkango,+ Ndipo mundiyankhe ndi kundipulumutsa ku nyanga za ng’ombe zamphongo zam’tchire.+ 22  Ndidzalengeza dzina lanu+ kwa abale anga.+ Ndidzakutamandani pakati pa mpingo.+ 23  Inu oopa Yehova, m’tamandeni!+ Inu nonse mbewu ya Yakobo, m’patseni ulemerero!+ Ndipo muopeni, inu nonse mbewu ya Isiraeli.+ 24  Pakuti iye sananyoze,+ Kapena kunyansidwa ndi nsautso ya munthu wosautsidwa.+ Ndipo sanam’bisire nkhope yake.+ Pamene anamulirira kuti amuthandize, iye anamva.+ 25  Chifukwa cha zimene mwachita ndidzakutamandani mumpingo waukulu.+ Ndidzakwaniritsa malonjezo anga pamaso pa anthu oopa iye.+ 26  Ofatsa adzadya ndi kukhuta.+ Ofunafuna Yehova adzamutamanda.+ Mitima yanu ikhale ndi moyo kosatha.+ 27  Anthu onse okhala kumalekezero a dziko lapansi adzakumbukira Yehova ndi kubwerera kwa iye.+ Ndipo mafuko onse a anthu a mitundu ina adzagwada pamaso panu.+ 28  Pakuti Yehova ndiye mfumu,+ Ndipo akulamulira mitundu.+ 29  Anthu onse a padziko lapansi onyada chifukwa cha chuma chawo adzadya ndi kuwerama.+ Onse otsikira kufumbi adzawerama pamaso pake,+ Ndipo palibe amene adzapulumutsa moyo wake.+ 30  Mbewu idzamutumikira.+ Adzalengeza za Yehova ku m’badwo wotsatira.+ 31  Adzafika ndi kunena za chilungamo chake,+ Adzauza anthu amene adzabadwe kuti iye ndiye wachita zimenezi.+

Mawu a M'munsi