Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 21:1-13

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide. 21  Inu Yehova, mfumu ikukondwera mu mphamvu zanu.+ Ndipo idzapitiriza kukondwera mu chipulumutso chanu.+   Mwaipatsa zokhumba za mtima wake,+ Ndipo simunaimane zokhumba za pakamwa pake.+ [Seʹlah.]   Munaidalitsa ndi kuipatsa zinthu zabwino,+ Ndipo pamutu pake munaika chisoti chachifumu chagolide woyengeka bwino.+   Mfumuyo inakupemphani moyo. Ndipo munaipatsadi,+ Munaipatsa masiku ochuluka kuti ikhale mpaka kalekale, ndithu mpaka muyaya.+   Ulemerero wake ndi waukulu m’chipulumutso chanu.+ Mwaipatsa ulemu ndi ulemerero.+   Mwaichititsa kukhala yodalitsika kwambiri mpaka muyaya.+ Mwaikondweretsa ndi kuisangalatsa pamaso panu.+   Pakuti mfumu imakhulupirira Yehova,+ Imakhulupirira kukoma mtima kosatha kwa Wam’mwambamwamba. Iyo siidzagwedezeka.+   Dzanja lanu lidzapeza adani anu onse.+ Dzanja lanu lamanja lidzapeza odana nanu.   Mudzawakhalitsa ngati oponyedwa mung’anjo yamoto pa nthawi ya kuonekera kwanu.+ Yehova adzawameza mu mkwiyo wake, ndipo moto udzawanyeketsa.+ 10  Mudzawononga ana awo kuwachotsa padziko lapansi,+ Ndipo ana awo mudzawachotsa pakati pa ana a anthu.+ 11  Pakuti akuchitirani zinthu zoipa.+ Alinganiza kuchita zinthu zimene sangazikwanitse.+ 12  Inu mudzawachititsa kutembenuka ndi kuthawa.+ Mudzachita zimenezi ndi zingwe za mauta amene mwakonzekera kuwalasa nawo pankhope.+ 13  Inu Yehova, mukhale wokwezeka mu mphamvu zanu.+ Tidzaimba ndi kutamanda mphamvu zanu.+

Mawu a M'munsi