Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Masalimo 20:1-9

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide. 20  Yehova akuyankheni pa tsiku la nsautso.+ Dzina la Mulungu wa Yakobo likutetezeni.+   Atumize thandizo kuchokera kumalo oyera.+ Akuchirikizeni ali ku Ziyoni.+   Akumbukire nsembe zanu zonse zimene munapereka monga mphatso.+ Alandire mafuta a nsembe zanu zopsereza.+ [Se′lah.]   Akupatseni zokhumba za mtima wanu,+ Ndipo akwaniritse zofuna zanu.+   Tidzafuula mokondwera chifukwa cha chipulumutso chanu,+ Tidzakweza mbendera zathu m’dzina la Mulungu wathu.+ Yehova akwaniritse zopempha zanu zonse.+   Tsopano ndadziwa kuti Yehova amapulumutsa wodzozedwa wake.+ Amamuyankha kuchokera kumwamba kwake koyera,+ Amamupulumutsa ndi dzanja lake lamanja lamphamvu zopulumutsa.+   Ena akunena za magaleta* ndipo ena akunena za mahatchi,*+ Koma ife tidzanena za dzina la Yehova Mulungu wathu.+   Anthu amenewo athyoka ndipo agwa,+ Koma ife tanyamuka ndipo taima chilili.+   Inu Yehova, pulumutsani mfumu!+ Tsiku limene tidzaitana, Mulungu adzatiyankha.+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Ena amati “mahosi” kapena “akavalo.”