Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Masalimo 2:1-12

2  N’chifukwa chiyani anthu a mitundu ina akuchita chipolowe,+ Ndiponso n’chifukwa chiyani mitundu ya anthu ikung’ung’udza za chinthu chopanda pake?+   Mafumu a dziko lapansi aima pamalo awo,+ Ndipo nduna zapamwamba zasonkhana pamodzi mogwirizana.+ Atero kuti alimbane ndi Yehova+ komanso wodzozedwa wake.+   Iwo akunena kuti: “Tiyeni tidule zomangira zawo,+ Ndipo titaye zingwe zawo kutali ndi ife!”+   Iye wokhala kumwamba+ adzaseka, Yehova adzawanyodola.+   Pa nthawiyo, adzawalankhula mu mkwiyo wake,+ Adzawasokoneza ataipidwa kwambiri.+   Ndipo adzanena kuti: “Inetu ndakhazika mfumu yanga+ Pa Ziyoni,+ phiri langa lopatulika.”+   Ndinene za lamulo la Yehova. Iye wandiuza kuti: “Iwe ndiwe mwana wanga,+ Lero, ine ndakhala bambo ako.+   Tandipempha,+ ndipo ndikupatsa mitundu ya anthu kukhala cholowa chako,+ Ndikupatsa dziko lonse lapansi kukhala lako.+   Mitunduyo udzaiswa ndi ndodo yachifumu yachitsulo,+ Udzaiphwanya ngati mbiya yadothi, n’kukhala zidutswazidutswa.”+ 10  Tsopano inu mafumu, sonyezani kuzindikira, Lolani kuti maganizo anu akonzedwe, inu oweruza a dziko lapansi.+ 11  Tumikirani Yehova mwamantha.+ Kondwerani ndipo nthunthumirani.+ 12  Psompsonani mwanayo+ kuopera kuti Mulungu angakwiye, Ndipo mungawonongeke ndi kuchotsedwa panjirayo.+ Pakuti mkwiyo wake umatha kuyaka mofulumira.+ Odala ndi onse amene akuthawira kwa iye.+

Mawu a M'munsi