Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 19:1-14

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide. 19  Zakumwamba zikulengeza ulemerero wa Mulungu.+ Ndipo m’mlengalenga mukufotokoza ntchito ya manja ake.+   Tsiku lililonse limanena mawu,+ Ndipo usiku uliwonse umasonyeza nzeru.+   Sizilankhula, kapena kutulutsa mawu. Mawu awo samveka.+   Zingwe zawo zoyezera zafika padziko lonse lapansi,+ Mawu awo amveka kumalekezero a dziko lapansi kumene kuli anthu.+ Kumwambako Mulungu wamangira dzuwa hema.+   Dzuwalo limaoneka ngati mkwati amene akutuluka m’chipinda chake,+ Limakondwa ngati mmene mwamuna wamphamvu amachitira akamathamanga m’njira.+   Limatuluka kuchokera kumalekezero ena a kumwamba, Ndi kuzungulira mpaka kumalekezero enanso.+ Palibe chinthu chilichonse chimene sichimva kutentha kwake.+   Chilamulo+ cha Yehova ndi changwiro,+ chimabwezeretsa moyo.+ Zikumbutso+ za Yehova ndi zodalirika,+ zimapatsa nzeru munthu wosadziwa zinthu.+   Malamulo+ ochokera kwa Yehova ndi olungama,+ amasangalatsa mtima.+ Chilamulo+ cha Yehova ndi choyera,+ chimatsegula maso.+   Kuopa+ Yehova n’koyera, ndipo kudzakhalapo kwamuyaya. Zigamulo+ za Yehova n’zolondola,+ ndipo pa mbali iliyonse zasonyezadi kuti ndi zolungama.+ 10  N’zolakalakika kuposa golide, kuposa golide wambiri woyengeka bwino.+ N’zotsekemera* kuposa uchi,+ inde kuposa uchi umene ukukha m’zisa.+ 11  Ndiponso mtumiki wanu amachenjezedwa nazo.+ Munthu wosunga zigamulozo amapeza mphoto yaikulu.+ 12  Ndani angazindikire yekha zinthu zimene walakwitsa?+ Mundikhululukire machimo amene ndachita mosadziwa.+ 13  Komanso mundiletse kuchita modzikuza, ine mtumiki wanu.+ Musalole kuti kudzikuza kundilamulire.+ Pamenepo ndidzakhala wopanda chifukwa,+ Ndipo ndidzakhalabe wopanda milandu yambiri yophwanya malamulo. 14  Mawu a pakamwa panga ndi kusinkhasinkha kwa mtima wanga,+ Zikukondweretseni, inu Yehova, Thanthwe langa+ ndi Wondiwombola.+

Mawu a M'munsi

Ena amati “n’zonzuna.”