Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 18:1-50

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la mtumiki wa Yehova, Davide, amene anauza Yehova mawu a m’nyimbo iyi pa tsiku limene Yehova anamulanditsa m’manja mwa adani ake onse komanso m’manja mwa Sauli.+ Iye anati: 18  Ndidzakukondani inu Yehova, mphamvu yanga.+   Yehova ndiye thanthwe langa, malo anga achitetezo ndiponso Wopereka chipulumutso kwa ine.+ Mulungu wanga ndiye thanthwe langa. Ine ndidzathawira kwa iye.+ Iye ndiye chishango changa, nyanga* yanga ya chipulumutso ndiponso ndiye malo anga okwezeka achitetezo.+   Ndidzaitanira pa Yehova, Iye woyenera kutamandidwa,+ Ndipo adzandipulumutsa kwa adani anga.+   Zingwe za imfa zinandikulunga,+ Chikhamu cha anthu opanda pake chinali kundiopseza.+   Zingwe za Manda zinandizungulira.+ Ndinayang’anizana ndi misampha ya imfa.+   Pa nthawi ya zowawa zanga ndinaitana Yehova, Ndinafuulira Mulungu wanga kuti andithandize.+ Iye anamva mawu anga ali m’kachisi wake.+ Pamenepo makutu ake anamva kulira kwanga kopempha thandizo.+   Dziko lapansi linayamba kugwedezekera uku ndi uku ndiponso kutekeseka.+ Maziko a mapiri anagwedezeka,+ Anagwedezekera uku ndi uku chifukwa Mulungu anakwiya.+   Utsi unatuluka m’mphuno mwake, ndipo moto wotuluka m’kamwa mwake unanyeketsa.+ Makala onyeka anatuluka mwa iye.   Iye anaweramitsa kumwamba n’kutsika.+ Mdima wandiweyani unali kunsi kwa mapazi ake. 10  Iye anafika atakwera pakerubi wouluka.+ Mulungu anali kuuluka mwaliwiro pamapiko a cholengedwa chauzimu.*+ 11  Kenako anapanga mdima kukhala malo ake obisalamo,+ Panali madzi akuda ndi mtambo wakuda, Zimene zinamuzungulira ngati msasa wake.+ 12  M’kuwala kochokera pamaso pake munatuluka mitambo yake,+ Munatulukanso matalala ndi makala onyeka a moto.+ 13  Ali kumwamba, Yehova anayamba kugunda ngati mabingu,+ Wam’mwambamwamba anayamba kutulutsa mawu ake,+ Anatulutsanso matalala ndi makala onyeka a moto. 14  Anayamba kuponya mivi kuti awabalalitse.+ Anaponya mphezi kuti awasokoneze.+ 15  Ndipo ngalande za pansi pa madzi zinaonekera,+ Maziko a dziko lapansi anakhala poonekera.+ Zinatero chifukwa cha kudzudzula kwanu, inu Yehova, chifukwa cha mphamvu ya mpweya wa m’mphuno mwanu.+ 16  Anatambasula dzanja lake kuchokera kumwamba ndi kunditenga,+ Anandivuula m’madzi akuya.+ 17  Anandilanditsa kwa mdani wanga wamphamvu,+ Anandilanditsa kwa odana nane chifukwa anali amphamvu kuposa ine.+ 18  Adaniwo anandifikira m’tsiku la tsoka langa,+ Koma Yehova anandichirikiza.+ 19  Ananditenga ndi kundiika pamalo otakasuka.+ Anandipulumutsa chifukwa anakondwera nane.+ 20  Yehova amandipatsa mphoto mogwirizana ndi chilungamo changa.+ Amandibwezera mogwirizana ndi kuyera kwa manja anga.+ 21  Pakuti ndasunga njira za Yehova,+ Sindinachoke kwa Mulungu wanga. Ndikanatero, ndikanachita chinthu choipa.+ 22  Zigamulo zake zonse zili pamaso panga,+ Ndipo malamulo ake sindidzawataya.+ 23  Ndidzakhalabe wopanda cholakwa pamaso pake,+ Ndipo ndidzayesetsa kupewa kuchita cholakwa.+ 24  Yehova andibwezere mogwirizana ndi chilungamo changa,+ Andibwezere mogwirizana ndi kuyera kwa manja anga pamaso pake.+ 25  Munthu wokhulupirika, mudzamuchitira mokhulupirika.+ Munthu wamphamvu  wopanda cholakwa,  mudzamuchitira mwachilungamo.+ 26  Kwa munthu wokhalabe woyera, mudzadzisonyeza kuti ndinu woyera,+ Kwa munthu wopotoka maganizo mudzadzisonyeza kuti ndinu wochenjera,+ 27  Chifukwa anthu osautsika mudzawapulumutsa,+ Koma anthu odzikweza mudzawatsitsa.+ 28  Pakuti inu Yehova mudzandiyatsira nyale yanga,+ Mulungu wanga adzandiunikira mu mdima.+ 29  Pakuti ndi thandizo lanu, ndingathamangitse gulu la achifwamba.+ Ndi thandizo la Mulungu wanga ndingakwere khoma.+ 30  Njira ya Mulungu woona ndi yangwiro.+ Mawu a Yehova ndi oyengeka bwino.+ Iye ndi chishango kwa onse othawira kwa iye.+ 31  Kodi pali Mulungu winanso woposa Yehova?+ Kodi pali thanthwe linanso loposa Mulungu wathu?+ 32  Mulungu woona Ndiye amandilimbitsa,*+ Ndipo adzasalaza njira yanga.+ 33  Iye adzachititsa mapazi anga kukhala aliwiro ngati a mbawala zazikazi,+ Ndipo adzandiimiritsabe pamalo okwezeka kwa ine.+ 34  Iye akuphunzitsa manja anga kumenya nkhondo,+ Ndipo manja anga akukunga uta wamkuwa.+ 35  Inu mudzandipatsa chishango chanu cha chipulumutso,+ Dzanja lanu lamanja lidzandichirikiza,+ Ndipo kudzichepetsa kwanu n’kumene kudzandikweza.+ 36  Mudzakulitsa malo opondapo mapazi anga,+ Ndipo mapazi anga sadzagwedezeka.+ 37  Ndidzathamangitsa adani anga ndi kuwapeza, Ndipo sindidzabwerera kufikira nditawawononga onse.+ 38  Ndidzawaphwanya zibenthuzibenthu kuti asadzukenso.+ Ndidzawapondaponda ndi mapazi anga.+ 39  Inu mudzandiveka mphamvu kuti ndithe kumenya nkhondo. Mudzakomola ondiukira.+ 40  Koma mudzachititsa adani anga kugonja* pamaso panga,+ Anthu odana nane kwambiri, ndidzawakhalitsa chete.+ 41  Adzafuula kupempha thandizo, koma sipadzapezeka wowapulumutsa,+ Adzafuulira Yehova, koma sadzawayankha.+ 42  Ndidzawapera kukhala ngati fumbi louluzika ndi mphepo.+ Ndidzawakhuthula ngati matope a mumsewu.+ 43  Inu mudzandipulumutsa kwa anthu a mtundu wanga onditola zifukwa.+ Mudzandiika kukhala mtsogoleri wa mitundu yonse.+ Anthu amene sindikuwadziwa adzanditumikira.+ 44  Anthu akangomva mphekesera chabe zokhudza ine, adzandimvera.+ Alendo adzabwera kwa ine akunthunthumira.+ 45  Alendo adzatha mphamvu, Ndipo adzatuluka m’malo awo achitetezo akunjenjemera.+ 46  Yehova ndi wamoyo.+ Lidalitsike Thanthwe langa.+ Mulungu wa chipulumutso changa akhale wokwezeka.+ 47  Mulungu woona ndiye Wobwezera adani anga.+ Iye amagonjetsa mitundu ya anthu ndi kuiika kunsi kwa mapazi anga.+ 48  Iye amandipulumutsa kwa adani anga olusa.+ Ndipo mudzandikweza pamwamba pa anthu amene amandiukira.+ Mudzandilanditsa kwa munthu wachiwawa.+ 49  N’chifukwa chake ndidzakutamandani, inu Yehova pakati pa mitundu.+ Ndipo ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.+ 50  Iye akuchita ntchito zazikulu za chipulumutso kwa mfumu yake,+ Ndipo akusonyeza kukoma mtima kosatha kwa wodzozedwa wake,+ kwa Davide ndi mbewu yake mpaka kalekale.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa 1Sa 2:1.
Kapena kuti “mapiko a mphepo.”
Mawu ake enieni, “amamangirira zolimba mphamvu m’chiuno mwanga.”
Kapena kuti “Mudzandipatsa kumbuyo kwa khosi la adani anga.”