Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 17:1-15

Pemphero la Davide. 17  Imvani dandaulo lolungama, inu Yehova. Mvetserani kulira kwanga kochonderera.+ Tcherani khutu ku pemphero langa limene likutuluka pamilomo yopanda chinyengo.+   Chiweruzo changa chichokere kwa inu.+ Maso anu aone kuwongoka mtima kwanga.+   Mwasanthula mtima wanga, mwandifufuza usiku,+ Ndipo mwandiyenga. Mudzaona kuti sindinaganizire kuchita choipa chilichonse.+ Pakamwa panga sipadzaphwanya malamulo.+   Kunena za ntchito za anthu, Ndakhala wosamala mwa kusunga mawu a pakamwa panu, kuti ndisatengere njira ya wachifwamba.+   Mapazi anga ayendebe m’njira zanu,+ Mmene sadzapunthwa ngakhale pang’ono.+   Ine ndikuitana pa inu, chifukwa mudzandiyankha, inu Mulungu.+ Tcherani khutu kwa ine. Imvani mawu anga.+   Sonyezani kukoma mtima kosatha mwa kuchita zodabwitsa,+ inu Mpulumutsi wa anthu othawira kwa inu, Amene akuthawa anthu ogalukira dzanja lanu lamanja.+   Ndisungeni monga mwana wa diso,+ Ndibiseni mumthunzi wa mapiko anu,+   Chifukwa cha anthu oipa amene akundipondereza. Adani a moyo wanga atsala pang’ono kundipeza.+ 10  Mitima yawo siimva chisoni,*+ Ndipo amalankhula modzikuza ndi pakamwa pawo.+ 11  Tsopano adaniwo atizungulira, kulikonse kumene tingapite.+ Akutiyang’anitsitsa kuti atigwetse.+ 12  Aliyense wa iwo akuoneka ngati mkango umene ukufunitsitsa kukhadzula nyama.+ Akuonekanso ngati mkango wamphamvu umene wabisalira nyama. 13  Nyamukani, inu Yehova, yang’anizanani naye maso ndi maso woipayo.+ M’gonjetseni. Pulumutsani moyo wanga kwa woipayo ndi lupanga lanu.+ 14  Ndipulumutseni kwa anthu ndi dzanja lanu, inu Yehova,+ Ndipulumutseni kwa anthu a m’nthawi* ino,+ amene gawo lawo lili m’moyo uno.+ Anthu amene mimba zawo mwazidzaza ndi chuma chanu chobisika,+ Amene ali ndi ana aamuna ochuluka,+ Ndipo amakundikira ana awo chuma.+ 15  Koma ine ndidzaona nkhope yanu m’chilungamo.+ Podzuka, ndidzakhutira pokuonani.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “adzikuta ndi mafuta awo omwe.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.