Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 16:1-11

Mikitamu* ya Davide. 16  Ndisungeni, inu Mulungu, pakuti ndathawira kwa inu.+   Ndauza Yehova kuti: “Inu ndinu Yehova. Ubwino wanga sungakupindulitseni,+   Koma ungapindulitse oyera amene ali padziko lapansi. Anthu aulemerero amenewo, ndi amene ndimakondwera nawo.”+   Zopweteka zimachuluka kwa anthu amene amati akaona mulungu wina, amamuthamangira.+ Ine sindidzatsanula nsembe zawo zachakumwa zothira magazi,+ Ndipo sindidzatchula dzina lawo ndi milomo yanga.+   Yehova ndiye gawo langa, gawo limene ndinapatsidwa,+ komanso chikho changa.+ Inu mukundisungira  bwino kwambiri cholowa changa.   Zingwe zoyezera zandigwera m’malo abwino.+ Ndithudi, gawo limene ndapatsidwa ndalivomereza.   Ndidzatamanda Yehova amene wandipatsa malangizo.+ Ndithudi, usiku impso zanga zandiwongolera.+   Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse.+ Popeza kuti ali kudzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.+   Choncho moyo wanga ukukondwera, ndipo ndidzakhala wosangalala.+ Komanso ndidzakhala wotetezeka.+ 10  Pakuti simudzasiya moyo wanga m’Manda.+ Simudzalola kuti wokhulupirika wanu aone dzenje.+ 11  Mudzandidziwitsa njira ya moyo.+ Chifukwa cha nkhope yanu, munthu adzakondwera mokwanira.+ Kudzanja lanu lamanja kuli chimwemwe mpaka muyaya.+

Mawu a M'munsi

“Mikitamu” ndi mawu amene anali kuwagwiritsa ntchito polemba nyimbo, koma tanthauzo lake lenileni silikudziwika.