Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 150:1-6

150  Tamandani Ya, anthu inu!+ Tamandani Mulungu m’malo ake oyera.+ Mutamandeni  m’mlengalenga mmene mumasonyeza mphamvu zake.+   Mutamandeni chifukwa cha ntchito zake zamphamvu.+ Mutamandeni mogwirizana ndi ukulu wake wosaneneka.+   Mutamandeni mwa kuliza lipenga la nyanga ya nkhosa.+ Mutamandeni ndi choimbira cha zingwe ndi zeze.+   Mutamandeni ndi maseche+ ndi gule wovina mozungulira.+ Mutamandeni ndi zoimbira za zingwe+ ndi chitoliro.+   Mutamandeni ndi chinganga cha mawu osangalatsa.+ Mutamandeni ndi chinganga cha mawu amphamvu.+   Chopuma chilichonse chitamande Ya.+ Tamandani Ya, anthu inu!+

Mawu a M'munsi