Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Masalimo 15:1-5

Nyimbo ya Davide. 15  Inu Yehova, ndani amene angakhale mlendo m’chihema chanu?+ Ndani angakhale  m’phiri lanu lopatulika?+   Ndi amene akuyenda mosalakwitsa zinthu,+ amene amachita chilungamo,+ Ndi kulankhula zoona mumtima mwake.+   Iye sanena miseche ndi lilime lake.+ Sachitira mnzake choipa,+ Ndipo satonza bwenzi lake lapamtima.+   Iye sagwirizana ndi munthu aliyense wonyansa,+ Koma anthu oopa Yehova amawalemekeza.+ Akalumbira kuchita zinthu zimene kenako zakhala zoipa kwa iye, sasintha malingaliro ake.+   Sapereka ndalama zake kuti alandire chiwongoladzanja,+ Ndipo salandira chiphuphu kuti akhotetse mlandu wa munthu wosalakwa.+ Wochita zinthu zimenezi, sadzagwedezeka konse.+

Mawu a M'munsi